Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 39:1-18

39  M’chaka cha 9 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 10,+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anafika ku Yerusalemu ndi kuzungulira mzindawo.+  M’chaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya, m’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9, anaboola mpanda wa mzindawo.+  Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindamo ndi kukhala pansi ku Chipata cha Pakati.+ Mayina a akalongawo anali Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.  Ndiyeno Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse ankhondo ataona adaniwo anayamba kuthawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo analowera njira ya kumunda wa mfumu,+ kukatulukira pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, n’kupitiriza kuthawa molowera ku Araba.+  Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+  Zitatero mfumu ya Babulo inapha+ ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona.+ Inaphanso akuluakulu onse a ku Yuda.+  Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga m’maunyolo amkuwa kuti apite naye ku Babulo.  Akasidi anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu onse.+ Iwo anagwetsanso mpanda wa Yerusalemu.+  Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+ 10  Ndiyeno ena mwa anthuwo, anthu onyozeka amene analibe kalikonse, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawasiya m’dziko la Yuda,+ ndipo pa tsiku limenelo anawapatsa minda ya mpesa ndi ntchito zokakamiza kuti azigwira.+ 11  Kuwonjezera pamenepo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo anapereka lamulo lokhudza Yeremiya kwa Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, kuti: 12  “Mtenge uzimuyang’anira ndipo usamuchitire choipa chilichonse.+ Koma uzimuchitira chilichonse chimene iye wanena.”+ 13  Pamenepo Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu pamodzi ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi, Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14  Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndi kumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake, kuti Yeremiyayo akakhale pakati pa anthu akwawo. 15  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene anali wotsekeredwa m’Bwalo la Alonda.+ Iye anamuuza kuti: 16  “Pita kwa Ebedi-meleki+ Mwitiyopiya ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndiugwetsera tsoka osati zinthu zabwino.+ Pa tsikulo zimene ndinanena zidzachitika iwe ukuona.”’+ 17  “‘Pa tsikulo ndidzakulanditsa+ ndipo sudzaperekedwa m’manja mwa anthu amene umawaopa,’+ watero Yehova. 18  “‘Pakuti ine ndidzakupulumutsa ndithu, ndipo sudzaphedwa ndi lupanga, koma udzapulumutsa moyo wako+ chifukwa chakuti wandikhulupirira,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu.”
Kapena kuti “mkulu wa azamatsenga (wolosera zam’tsogolo, wopenda nyenyezi), mkulu wa akuluakulu.”