Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 37:1-21

37  Ndiyeno Mfumu Zedekiya mwana wa Yosiya, amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anamuika kukhala mfumu m’dziko la Yuda, anayamba kulamulira m’malo mwa Koniya mwana wa Yehoyakimu.  Koma Zedekiyayo, atumiki ake ndi anthu a m’dzikoli sanamvere mawu amene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya.+  Mfumu Zedekiya inatumiza Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya mwana wa Maaseya+ wansembe kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga wakuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.”+  Yeremiya anali kukhala mwaufulu pakati pa anthu+ chifukwa anali asanamutsekere m’ndende.  Ndiyeno gulu lankhondo la Farao linabwera kuchokera ku Iguputo.+ Akasidi amene anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu atamva zimenezi anachoka ku Yerusalemu.+  Kenako Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu inu mukauze mfumu ya Yuda imene yakutumani kuno kudzafunsira uthenga wa Mulungu kwa ine+ kuti: “Taonani! Gulu lankhondo la Farao limene likubwera kwa anthu inu kuti likuthandizeni lidzabwerera kwawo ku Iguputo.+  Ndipo Akasidi adzabweranso ndithu kudzamenyana ndi mzinda uno, kuulanda ndi kuutentha ndi moto.”+  Yehova wanena kuti: “Musadzinyenge+ pomanena kuti, ‘Akasidi amenewa samenyana nafe, achoka ndithu,’ chifukwa sachoka ayi. 10  Pakuti ngakhale anthu inu mutapha gulu lonse lankhondo la Akasidi amene akumenyana nanu+ ndipo pangotsala amuna ovulala kwambiri pakati pawo,+ aliyense wa amenewo adzadzuka muhema wake ndi kubwera kudzatentha mzinda uno.”’” 11  Ndiyeno gulu lankhondo la Akasidi litabwerera kuchoka ku Yerusalemu+ chifukwa cha gulu lankhondo la Farao,+ 12  Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita kudziko la Benjamini kuti akalandire malo ake pakati pa anthu ake. 13  Atafika pa Chipata cha Benjamini,+ anakumana ndi mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya. Nthawi yomweyo Iriya anagwira mneneri Yeremiya ndi kunena kuti: “Ukuthawira kwa Akasidi!” 14  Yeremiya anamuyankha kuti: “Zabodza zimenezo!+ Ine sindikuthawira kwa Akasidi.” Koma Iriya sanamumvere. Choncho iye anagwirabe Yeremiya ndi kumubweretsa kwa akalonga. 15  Pamenepo akalonga+ anamukwiyira kwambiri Yeremiya+ ndipo anamumenya+ ndi kumutsekera m’ndende m’nyumba ya Yehonatani+ mlembi, pakuti nyumba yake ndi imene anaisandutsa ndende.+ 16  Yeremiya atalowa m’ndende ya pansiyo,+ m’kachipinda ka m’ndendemo, anakhala mmenemo kwa masiku ambiri. 17  Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya. Atabwera naye, mfumuyo inayamba kumufunsa mafunso m’nyumba mwake pamalo obisika.+ Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Pamenepo Yeremiya anayankha kuti: “Inde alipo!” Ndiyeno Yeremiya ananenanso kuti: “Inuyo mudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Babulo!”+ 18  Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti: “Kodi ineyo ndakulakwirani chiyani pamodzi ndi atumiki anu ndiponso anthu onse, kuti munditsekere m’ndende? 19  Tsopano ali kuti aneneri anu amene anali kulosera kwa inu ponena kuti, ‘Mfumu ya Babulo sidzabwera kudzamenyana ndi anthu inu ndiponso kudzamenyana ndi dzikoli’?+ 20  Tsopano ndimvereni chonde, mbuyanga mfumu. Chonde, mverani pempho langa lakuti mundikomere mtima.+ Musandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ mlembi, chifukwa ndingakafere kumeneko.”+ 21  Chotero Mfumu Zedekiya inalamula kuti atsekere Yeremiya m’Bwalo la Alonda ndipo anali kumupatsa mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo. Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

Mawu a M'munsi