Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 33:1-26

33  Yeremiya atamutsekera m’Bwalo la Alonda,+ Yehova analankhula naye kachiwiri kuti:  “Yehova Wopanga+ dziko lapansi, Yehova Woumba+ dzikoli ndi kulikhazikitsa.+ Mulungu amene dzina lake ndi Yehova,+ wanena kuti,  ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani.+ Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+  “Pakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba za mumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda zimene zagwetsedwa podziteteza ku ziunda zomenyerapo nkhondo ndiponso ku lupanga la adani.+  Wanenanso mawu okhudza amuna amene akubwera kudzamenyana ndi Akasidi, ndiponso okhudza malo amene adzaza ndi mitembo ya amuna amene wawapha chifukwa cha mkwiyo wake waukulu,+ amenenso ali oipa kwambiri moti iye wausiya mzindawu chifukwa cha kuipa kwa anthu amenewo.+  Iye wanena kuti: ‘Ine ndichiritsa anthu a mumzindawu ndi kuwapatsa thanzi labwino.+ Ndiwachiritsa ndi kuwapatsa mtendere wochuluka ndi choonadi.+  Ndibwezeretsa anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo ndiwalimbitsa kuti akhale ngati mmene analili poyamba.+  Ndiwayeretsa ku zolakwa zawo zonse zimene anachimwa nazo pamaso panga,+ ndipo ndiwakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nazo ndi kuphwanya nazo malamulo anga.+  Mzindawu udzakhala ndi dzina limene lidzandikondweretsa,+ dzina lochititsa kuti nditamandidwe ndi kulandira ulemerero pakati pa mitundu yonse ya padziko lapansi imene idzamva za zinthu zabwino zimene ndikuwachitira.+ Anthu a mitundu inawo adzachita mantha+ ndi kunjenjemera+ chifukwa cha zinthu zabwino ndi mtendere wonse umene ndikubweretsa pamzindawu.’”+ 10  “Yehova wanena kuti, ‘Anthu inu mudzanena za dziko lino kuti ndi lopanda pake chifukwa mulibe anthu ndi ziweto. Mudzanena zimenezi za mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu imene yawonongeka,+ moti mulibe anthu ndipo simukukhala munthu aliyense ngakhale ziweto.+ 11  M’malo amenewa mudzamveka mawu achikondwerero ndi achisangalalo.+ Mudzamveka mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi, ndi mawu a anthu onena kuti: “Tamandani Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndi wabwino.+ Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale!”’+ “‘Anthuwo azidzabweretsa nsembe yoyamikira kunyumba ya Yehova,+ pakuti ndidzabwezeretsa anthu a m’dzikoli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’+ watero Yehova.” 12  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘M’dziko lino lopanda pake, lopanda anthu ndi lopanda ziweto+ ndi mizinda yake yonse, mudzakhala malo odyetserako ziweto kumene abusa adzalola ziweto zawo kugona pansi.’+ 13  “Yehova wanena kuti, ‘Ziweto zidzadutsa pansi pa dzanja la munthu woziwerenga+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa,+ m’mizinda ya kum’mwera,+ m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu+ ndi m’mizinda ya Yuda.’”+ 14  “‘Taonani! Masiku adzafika+ pamene ndidzakwaniritsa lonjezo langa+ lokhudza nyumba ya Isiraeli+ ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova. 15  M’masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira yolungama+ ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo m’dzikoli.+ 16  M’masiku amenewo, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu adzatchedwa kuti, Yehova Ndiye Chilungamo Chathu.’”+ 17  “Yehova wanena kuti, ‘M’nyumba ya Davide simudzasowa munthu wokhala pampando wachifumu wa nyumba ya Isiraeli.+ 18  Ndipo ponena za ansembe achilevi, pakati pawo sindidzasowa mwamuna wopereka nsembe zopsereza zathunthu, nsembe yambewu yofukiza komanso nsembe zina nthawi zonse.’”+ 19  Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 20  “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale usana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti usana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+ 21  ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi atumiki anga, ansembe achilevi.+ 22  Ine ndidzachulukitsa mbewu ya Davide mtumiki wanga ndi Alevi amene akunditumikira.+ Ndidzawachulukitsa mofanana ndi makamu akumwamba amene sangathe kuwerengedwa ndiponso mofanana ndi mchenga umene munthu sangathe kuuyeza.’”+ 23  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Yeremiya kuti: 24  “Kodi sunamve zimene ena mwa anthu awa akunena kuti, ‘Mabanja awiri amene Yehova wasankha,+ adzawakananso’? Adani akuchitira anthu anga zachipongwe+ ndipo sakuwaonanso ngati mtundu wa anthu. 25  “Yehova wanena kuti, ‘Monga momwedi ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale usana ndi usiku,+ malamulo anga akumwamba ndi dziko lapansi,+ 26  momwemonso sindidzakana mbewu ya Yakobo ndi mbewu ya Davide mtumiki wanga,+ kuti pakati pa mbewu yake nditengepo olamulira mbewu ya Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Pakuti ndidzasonkhanitsa onse amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+

Mawu a M'munsi