Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 30:1-24

30  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.+  Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+  Awa ndi mawu amene Yehova wauza Isiraeli ndi Yuda.  Yehova wanena kuti: “Ife tamva phokoso la anthu amene akunjenjemera. Iwo agwidwa ndi mantha+ ndipo palibe mtendere.  Anthu inu, funsani kuti mudziwe ngati mwamuna angabale mwana.+ N’chifukwa chiyani mwamuna aliyense wamphamvu akuoneka atagwira manja m’chiuno ngati mkazi amene akubala mwana? N’chifukwa chiyani nkhope zawo zonse zafooka?+  Kalanga ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu+ moti palibe lofanana nalo.+ Limeneli ndi tsiku la masautso kwa Yakobo.+ Koma adzapulumuka m’masautso amenewa.”  “Pa tsikuli ndidzathyola goli ndi kulichotsa m’khosi lanu. Ndidzadula zingwe zimene akumangani nazo,+ moti alendowo sadzagwiritsanso ntchito Yakobo monga wantchito wawo,” watero Yehova wa makamu.  “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu+ imene ndidzakuutsirani.”+ 10  “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+ 11  “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+ 12  Yehova wanena kuti: “Sudzachira kuvulala kwako.+ Chilonda chako cha mkwapulo ndi chosachiritsika.+ 13  Palibe amene akuchonderera kuti chilonda chako chipole.+ Palibe njira iliyonse yokuchiritsira ndipo palibe mankhwala amene angakuthandize.+ 14  Achigololo onse amene anali kukukonda kwambiri akuiwala.+ Iwo sakukufunafunanso. Ndakumenya ndi mkwapulo+ ngati mdani ndipo ndakulanga ngati munthu wankhanza+ chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako.+ Machimo ako achuluka kwambiri.+ 15  N’chifukwa chiyani ukulira pamene wadzivulaza mwadala?+ Ululu wako ndi wosachiritsika chifukwa zolakwa zako zachuluka ndipo machimo ako ndi ochuluka kwambiri.+ Ine ndakuchitira zimenezi. 16  Choncho, onse okuwononga adzawonongedwa,+ ndipo adani ako onse adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Amene akulanda katundu wako nawonso adzalandidwa katundu wawo. Onse ofunkha zinthu zako nawonso zinthu zawo zidzafunkhidwa.”+ 17  “Ndidzakubwezeretsa mwakale ndipo ndidzachiritsa zilonda zako za mkwapulo,”+ watero Yehova. “Iwo anakutcha kuti mkazi wothamangitsidwa ndipo anali kunena kuti:+ ‘Ameneyu ndi Ziyoni ndipo palibe amene akumufunafuna.’”+ 18  Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu a m’mahema a Yakobo+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pachiunda chake+ ndipo nsanja yokhalamo idzakhala pamalo ake oyenera.+ 19  Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+ Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+ Ndidzachulukitsa chiwerengero chawo moti sadzakhala kagulu kakang’ono ka anthu.+ 20  Ana ake aamuna adzabwerera mwakale ndipo khamu la anthu ake lidzakhazikika pamaso panga.+ Ndidzalanga onse omupondereza.+ 21  Munthu wotchuka adzachokera mwa iye+ ndipo pakati pa anthu ake padzatuluka wolamulira.+ Ndidzamulola kundiyandikira ndipo adzabwera kwa ine.”+ “Tsopano uyu ndani amene wapereka mtima wake ngati chikole kuti ayandikire kwa ine?”+ watero Yehova. 22  “Inu mudzakhaladi anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.”+ 23  Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova yawomba. Mkwiyo wake wawomba ngati kamvulumvulu wosakaza.+ Wawomba pamitu ya anthu oipa.+ 24  Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi.+

Mawu a M'munsi