Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 3:1-25

3  Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.” Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+ Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+  Kweza maso ako ndi kuona njira zodutsidwadutsidwa.+ Ndi pamalo ati pamene amuna sanakugonerepo?+ Unali kukhala m’mbali mwa njira kudikirira okondedwa ako, ngati mmene Mluya amakhalira m’chipululu. Ukuipitsa dzikoli ndi zochita zako zauhule komanso kuipa kwako.+  Choncho mvula yamvumbi yasiya kugwa, ndipo mvula yomalizira siinagwe.+ Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.* Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+  Tsopano wayamba kundiitana kuti, ‘Atate wanga,+ ndinu bwenzi langa lapamtima kuyambira pa unyamata wanga.+  Kodi mukhala wokwiya mpaka kalekale?* Kapena kodi muzingoyang’anira machimo athu mpaka muyaya?’+ Taona! Iwe wanena ndi kuchita zinthu zoipa ndipo wapambana.”+  Yehova anapitiriza kulankhula nane m’masiku a Mfumu Yosiya kuti: “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita?+ Akupita kuphiri lililonse lalitali+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira kuti akachite uhule kumeneko.+  Pambuyo poti wachita zinthu zonsezi, ine ndinamupempha mobwerezabwereza kuti abwerere kwa ine, koma iye sanabwerere. Ndipo Yuda anali kungoyang’anitsitsa zimene m’bale wake wachinyengoyo anali kuchita.+  Nditaona zimenezo, ndinam’pitikitsa+ ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha chifukwa chakuti Isiraeli wosakhulupirikayu anachita chigololo. Koma Yuda amene ndi m’bale wake wochita zachinyengo sanachite mantha ndipo nayenso anayamba kuchita uhule.  Iye anayamba kuchita uhule chifukwa choona nkhani imeneyi mopepuka. Anali kuipitsa dzikolo+ ndi kuchita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+ 10  Ngakhale kuti m’bale wake Yuda amene anali wochita zachinyengoyo anaona zonsezi, iye sanabwerere kwa ine ndi mtima wake wonse+ koma anangobwerera mwachiphamaso,’+ watero Yehova.” 11  Yehova anapitiriza kundiuza kuti: “Isiraeli wosakhulupirikayo wakhala wolungama kuposa Yuda wochita zachinyengoyo.+ 12  Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto kuti: “‘Yehova wanena kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyang’anani mokwiya anthu inu+ pakuti ndine wokhulupirika,”+ watero Yehova. “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.+ 13  Koma ganizirani zolakwa zanu chifukwa mwaphwanya malamulo a Yehova Mulungu wanu. Anthu inu simunamvere mawu anga, koma munapitiriza kupanga njira zambirimbiri zopita kwa anthu achilendo+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira,” watero Yehova.’” 14  “Bwererani inu ana opanduka,”+ watero Yehova. “Ine ndakhala mwamuna wanu anthu inu.+ Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mu fuko lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+ 15  Ndidzakupatsani abusa amene mtima wanga wakonda+ ndipo iwo adzakuthandizani kudziwa zinthu zambiri ndiponso kumvetsa bwino zinthu.+ 16  Pamenepo mudzabalana ndi kuchuluka m’dzikoli masiku amenewo,” watero Yehova.+ “Iwo sadzafuulanso kuti, ‘Likasa la pangano la Yehova!’ Sadzaliganiziranso m’mitima yawo, kulikumbukira,+ kapena kulilakalaka ndipo sadzapanganso likasa lina. 17  Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+ 18  “M’masiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli,+ ndipo onse adzatuluka m’dziko la kumpoto ndi kulowa m’dziko limene ndinapereka kwa makolo anu monga cholowa chawo.+ 19  Ine ndanena kuti, ‘Mokondwera ndinakuikani pakati pa ana anga ndi kukupatsani dziko labwino,+ cholowa chimene mitundu yambiri ya anthu imachisirira!’ Ndipo ndinanenanso kuti, ‘Anthu inu mudzandiitana kuti, “Atate wanga!”+ ndipo mudzandilondola osabwerera.’ 20  ‘Ndithudi, monga mmene mkazi amasiyira mwamuna wake+ mwachinyengo, inunso a m’nyumba ya Isiraeli mwandichitira zachinyengo,’+ watero Yehova.” 21  Panjira zodutsidwadutsidwa pamveka mawu a ana a Isiraeli, kulira ndi kuchonderera kwawo. Pakuti iwo akhotetsa njira zawo+ ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+ 22  “Bwererani, inu ana opanduka.+ Ndidzachiritsa kusakhulupirika kwanu.”+ “Ife tabwerera! Tabwera kwa inu, pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ 23  Ndithudi, zitunda ndi chipwirikiti chimene chimachitika m’mapiri+ ndiko kupembedza kwachinyengo.+ Kunena zoona chipulumutso cha Isiraeli chili mwa Yehova Mulungu wathu.+ 24  Chinthu chochititsa manyazi+ chadya ntchito yolemetsa ya manja a makolo athu kuyambira tili anyamata. Chadya nkhosa zawo, ng’ombe zawo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. 25  Tagona pansi mwamanyazi ndipo manyazi athuwo akupitiriza kutiphimba.+ Zimenezi zakhala choncho chifukwa chakuti ifeyo ndi makolo athu, tachimwira Yehova Mulungu wathu+ ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu kuyambira tili anyamata mpaka lero.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “uli ndi nkhope ya mkazi wochita uhule.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.