Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 27:1-22

27  Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti akanene mawu akuti:  “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira ndiponso magoli,+ ndipo uzivale m’khosi mwako.+  Kenako, uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu, mfumu ya ana a Amoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene akubwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda.  Ukatero, uwalamule kuti akauze ambuye awo kuti: “‘“Mukauze ambuye anu kuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti,  ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+  Tsopano ndapereka mayiko onsewa m’manja mwa mtumiki wanga+ Nebukadinezara, mfumu ya Babulo.+ Ndamupatsanso nyama zakutchire kuti zimutumikire.+  Choncho mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo, mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pamenepo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamugwiritsa ntchito ngati wantchito wawo.’+  “‘“‘Ndiyeno mtundu uliwonse wa anthu ndi ufumu umene sudzatumikira Nebukadinezara mfumu ya Babulo, umenenso sudzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo, ine ndidzaulanga ndi lupanga, njala yaikulu ndi mliri+ kufikira nditaufafaniza kudzera mwa Nebukadinezara,’+ watero Yehova.  “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri, ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+ 10  Pakuti anthu amenewa akulosera monama kwa inu. Ndipo mukawamvera mudzatengedwa kuchoka m’dziko lanu kupita kudziko lakutali. Ine ndidzakubalalitsani ndipo inu mudzatheratu.+ 11  “‘“‘Mtundu wa anthu umene udzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira, ndidzauchititsa kukhala mwamtendere m’dziko lawo, ndipo adzalima minda ndi kukhalabe m’dzikomo,’ watero Yehova.”’”+ 12  Zedekiya mfumu ya Yuda ndinamuuza mawu onsewa kuti: “Ikani makosi anu m’goli la mfumu ya Babulo ndi kuitumikira. Mutumikire mfumuyo ndi anthu ake, kuti mukhalebe ndi moyo.+ 13  Kodi iweyo ndi anthu ako muferenji ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri?+ Izi ndi zimene Yehova wanena kuti zidzachitikira mtundu umene sukutumikira mfumu ya Babulo. 14  Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+ 15  “‘Ine sindinawatume,’ watero Yehova, ‘koma iwo akulosera m’dzina langa monama, ndipo mukawamvera ndidzakubalalitsani.+ Inu pamodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inuwo mudzatha.’” 16  Ndiyeno ndinalankhula ndi ansembe ndi anthu ena onsewa kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya za m’nyumba ya Yehova zibwezedwa kuchokera ku Babulo posachedwapa!” Pakuti iwo akulosera kwa inu monama.+ 17  Musawamvere. Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mukhale ndi moyo.+ Kodi mzinda uwu ukhale bwinja chifukwa chiyani? 18  Koma ngati iwo ndi aneneri, ndipo Yehova wawauza mawu, iwo achonderere kwa Yehova wa makamu kuti ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babulo.’ 19  “Yehova wa makamu wanena mawu okhudza zipilala, thanki ya madzi,* zotengera zamawilo ndi ziwiya zotsala mumzinda uwu, 20  zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anasiya pamene anatenga Yekoniya mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu. 21  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza ziwiya zimene zinatsala m’nyumba ya Yehova, m’nyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu kuti, 22  ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo ndipo zidzakhala kumeneko kufikira ine nditazikumbukira,” watero Yehova. “Ndipo ndidzazibweretsa ndi kuzibwezeretsa pamalo ano.”’”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “nyanja.”