Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 26:1-24

26  Kuchiyambi kwa ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panafika mawu ochokera kwa Yehova akuti:  “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire m’bwalo la nyumba ya Yehova,+ ndipo anthu onse amene akubwera kudzalambira panyumba ya Yehova ukawauze zimene zidzachitikira mizinda yonse ya Yuda. Ukawauze mawu onse amene ndidzakulamula kuti uwauze.+ Usachotsepo mawu ngakhale amodzi.  Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa.+ Pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.  Choncho uwauze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ngati simudzandimvera mwa kutsatira chilamulo chimene ndakupatsani,+  komanso kumvera mawu a atumiki anga aneneri amene ndikuwatumiza kwa inu, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwatumiza, amene inu simunawamvere,  pamenepo ine ndidzachititsa nyumba iyi kukhala ngati nyumba ya ku Silo.+ Ndipo mzinda uwu ndidzausandutsa chinthu chotembereredwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.’”’”+  Choncho ansembe, aneneri ndi anthu onse anayamba kumvetsera pamene Yeremiya anali kulankhula mawu amenewa m’nyumba ya Yehova.+  Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira ndi kunena kuti: “Ukufa basi.+  N’chifukwa chiyani wanenera m’dzina la Yehova kuti, ‘Nyumba iyi idzafanana ndi nyumba ya ku Silo+ ndipo mzinda uwu udzawonongedwa moti simudzapezeka aliyense wokhalamo’?” Pamenepo anthu onse anali kubwera ndi kuzungulira Yeremiya m’nyumba ya Yehova. 10  Kenako akalonga a Yuda anamva mawu amenewa ndipo anakwezeka kuchokera kunyumba ya mfumu kupita kunyumba ya Yehova.+ Kumeneko anakhala pansi pachipata chatsopano cha nyumba ya Yehova. 11  Pamenepo ansembe ndi aneneri anayamba kuuza akalongawo ndi anthu onse kuti: “Munthu uyu akuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa chakuti wanenera za mzinda uwu monga mmene mwamvera ndi makutu anu.”+ 12  Atatero, Yeremiya anauza akalonga onse ndi anthu onse kuti: “Yehova ndi amene anandituma kuti ndidzanenere mawu onse amene mwamva okhudza nyumba iyi ndi mzinda uwu.+ 13  Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino+ ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake pa tsoka limene wanena kuti akugwetserani.+ 14  Kunena za ine, ndilitu m’manja mwanu.+ Ndichiteni zimene mukuona kuti n’zabwino ndi zoyenera. 15  Koma mudziwe kuti, mukandipha mupalamula mlandu wamagazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Mlanduwo ukhala pa inuyo, pamzindawu ndi pa anthu onse okhala mumzindawu chifukwa kunena zoona, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onsewa.”+ 16  Zitatero, akalonga+ ndi anthu onse anauza ansembe ndi aneneriwo kuti: “Munthu uyu sakuyenera chiweruzo cha imfa+ chifukwa walankhula nafe m’dzina la Yehova Mulungu wathu.”+ 17  Ndiyeno akuluakulu ena a anthu a m’dzikomo anaimirira ndi kuyamba kuuza mpingo wonse wa anthuwo kuti:+ 18  “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda. Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+ 19  Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova? Kodi atatero, Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawagwetsera? Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu. 20  “Panalinso munthu wina amene anali kunenera m’dzina la Yehova. Iyeyu anali Uliya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-yearimu. Iye anali kunenera zimene zidzachitikira mzinda uwu ndi dziko ili mogwirizana ndi mawu onse a Yeremiya. 21  Ndiyeno Mfumu Yehoyakimu, asilikali ake onse amphamvu ndi akalonga onse anamva mawu amene Uliya anali kunena. Pamenepo mfumu inakonza zoti imuphe. Uliya atamva zimenezo, nthawi yomweyo anachita mantha ndipo anathawira ku Iguputo. 22  Koma Mfumu Yehoyakimu inatumiza Elinatani, mwana wa Akibori ndi amuna ena ku Iguputo. 23  Kumeneko anthuwo anagwira Uliya ndi kubwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inapha Uliya ndi lupanga+ ndi kutaya mtembo wake m’manda a anthu wamba.” 24  Koma Ahikamu, mwana wa Safani anali kuteteza Yeremiya kuti anthu asamuphe.

Mawu a M'munsi