Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 24:1-10

24  Ndiyeno Yehova anandisonyeza madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandisonyeza zimenezi Nebukadirezara mfumu ya Babulo atatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri+ ndi omanga makoma achitetezo kuchokera ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+  Nkhuyu zimene zinali m’dengu limodzi zinali zabwino kwambiri ngati nkhuyu zoyamba kucha.+ Koma nkhuyu zimene zinali m’dengu lina zinali zoipa kwambiri moti munthu sakanatha kuzidya chifukwa cha kuipa kwake.  Pamenepo Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Yeremiya?” Ndipo ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nkhuyu. Nkhuyu zabwino n’zabwino kwambiri, ndipo nkhuyu zoipa n’zoipa kwambiri moti munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake.”+  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu otengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo kudziko la Akasidi ndidzawaona ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawatumiza kudziko la Akasidi+ kuchoka m’dziko lino m’njira yabwino.+  Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino,+ ndipo ndidzawabwezeretsa kudziko lino.+ Pamenepo ndidzawalimbitsa, osati kuwapasula. Ndidzawabzala, osati kuwazula.+  Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo pakuti adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+  “‘Chotero mofanana ndi nkhuyu zoipa zija zimene munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake,+ Yehova wanena kuti: “Momwemonso ndidzapereka Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake ndi anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira m’dzikoli,+ komanso anthu okhala m’dziko la Iguputo.+  Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho, chifukwa cha masoka aakulu amene ndidzawagwetsera.+ Anthu a mitundu ina adzawatonza, kuwayesa chosereula, kuwanyoza+ ndipo adzakhala otembereredwa+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsirako.+ 10  Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+

Mawu a M'munsi