Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 22:1-30

22  Yehova wanena kuti: “Pita kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndipo kumeneko ukanene mawu awa.  Ukanene kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mfumu ya Yuda amene mwakhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mumve mawu amenewa inuyo, atumiki anu komanso anthu anu amene amalowa pazipata izi.+  Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo, muzilanditsa munthu amene anthu achinyengo akufuna kumulanda katundu wake. Musachitire nkhanza mlendo aliyense wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye* kapena mkazi wamasiye.+ Musawachitire zachiwawa.+ Musakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa m’dziko lino.+  Mukatsatiradi mawu amenewa, pazipata za nyumba iyi padzalowa mafumu okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mfumu iliyonse idzalowa pamodzi ndi atumiki ake ndi anthu ake atakwera magaleta ndi mahatchi.”’+  “‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pali ine mwini+ kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ watero Yehova.+  “Ponena za nyumba ya mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Kwa ine, iwe uli ngati Giliyadi ndiponso ngati nsonga ya phiri la ku Lebanoni.+ Ndithudi ndidzakusandutsa chipululu+ ndipo m’mizinda iyi simudzapezeka aliyense wokhalamo.+  Ndidzakuutsira owononga+ ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi zida zake.+ Iwo adzadula mitengo yako yabwino kwambiri ya mkungudza+ ndi kuigwetsera pamoto.+  Anthu a mitundu yambiri adzadutsa pafupi ndi mzinda uwu ndipo adzafunsana kuti: “N’chifukwa chiyani Yehova anachitira mzinda waukuluwu zinthu zoterezi?”+  Ndipo adzanena kuti: “Anauchitira zimenezi chifukwa chakuti anthu a mumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo+ ndi kuyamba kulambira milungu ina ndi kuitumikira.”’+ 10  “Munthu wakufa musamulire kapena kumumvera chisoni anthu inu.+ Lirani munthu amene watengedwa kupita ku ukapolo chifukwa sadzabwererakonso ndipo sadzaonanso dziko lakwawo. 11  Ponena za Salumu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene akulamulira m’malo mwa bambo ake Yosiya,+ amene anachoka m’dziko lino kupita ku ukapolo, Yehova wanena kuti, ‘Sadzabwereranso kwawo, 12  chifukwa akafera kudziko laukapolo kumene amutengera ndipo dziko lino sadzalionanso.’+ 13  “Tsoka amene akumanga nyumba yake+ komanso zipinda zake zam’mwamba mopanda chilungamo mwa kugwiritsa ntchito anthu kwaulere, osawapatsa malipiro.+ 14  Iye akunena kuti, ‘Ndimanga nyumba yaikulu ndi zipinda zikuluzikulu zam’mwamba.+ Ndikulitsa mawindo ake ndipo ndiyala matabwa a mkungudza+ ndi kupaka utoto wofiira.’+ 15  Kodi upitiriza kulamulira chifukwa chakuti matabwa a mkungudzawa akukuchititsa kukhala wapamwamba kuposa ena? Kodi bambo ako sanali kudya, kumwa ndi kuchita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo?+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinawayendera bwino.+ 16  Anali kunenera mlandu anthu osautsika ndi osauka.+ Chifukwa chochita zimenezi zinthu zinayenda bwino. ‘Kodi sanachite zimenezi chifukwa chakuti anali kundidziwa?’ watero Yehova. 17  ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’ 18  “Choncho ponena za Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sadzamulira monga mmene anthu amachitira kuti: “Kalanga ine m’bale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!” Sadzamulira kuti: “Kalanga ine mbuye wanga! Kalanga ine, onani mmene ulemerero wake wathera!”+ 19  Adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.+ Adzamukoka kudutsa naye pazipata za Yerusalemu ndi kukamutaya kunja.’+ 20  “Pita ku Lebanoni+ kuti ukalire kumeneko, ndipo ukafuule ku Basana.+ Ukalirenso ku Abarimu+ chifukwa amene anali kukukonda kwambiri agonjetsedwa.+ 21  Ndinalankhula nawe pamene unali pa ufulu,+ koma iwe unandiyankha kuti, ‘Sindidzamvera.’+ Wakhala ukuchita zimenezi kuyambira uli wachinyamata, moti sunamvere mawu anga.+ 22  Mphepo idzaweta abusa ako onse+ ndipo anthu onse amene akukukonda kwambiri adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Pa nthawi imeneyo udzachita manyazi ndipo udzanyazitsidwadi chifukwa cha tsoka limene lidzakugwere.+ 23  Inu okhala mu Lebanoni,+ amene mukuwetedwa m’nyumba zamitengo ya mkungudza,+ mudzausadi moyo zowawa za pobereka zikadzakugwerani,+ mukadzamva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.”+ 24  “‘Pali ine, Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, ‘ngakhale iwe Koniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, utakhala mphete yodindira+ kudzanja langa lamanja, ndidzakuvula!+ 25  Ndipo ndidzakupereka m’manja mwa anthu ofunafuna moyo wako,+ m’manja mwa amene umawaopa, m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ndiponso m’manja mwa Akasidi.+ 26  Iwe ndi mayi ako+ amene anakubereka, ndidzakuponyani kudziko lina limene anthu inu simunabadwireko ndipo mudzafera kumeneko.+ 27  Ndidzakuponyani kudziko limene mitima yanu idzalakalaka kubwererako, koma simudzabwererako.+ 28  Kodi munthu uyu Koniya+ wangokhala chiwiya chonyozeka, chophwanyika+ komanso chosasangalatsa?+ N’chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuyenera kugwetsedwa ndi kuponyedwa kudziko limene sakulidziwa?’+ 29  “Iwe dziko lapansi, dziko lapansi, dziko lapansi, tamvera mawu a Yehova.+ 30  Yehova wanena kuti, ‘Lembani kuti munthu uyu alibe ana,+ munthu wamphamvu amene zinthu sizidzamuyendera bwino m’masiku a moyo wake. Pakuti mwa ana ake onse, palibe ndi mmodzi yemwe amene zinthu zidzamuyendera bwino.+ Palibe ngakhale mmodzi amene adzakhala pampando wachifumu wa Davide+ ndi kulamulira mu Yuda.’”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”