Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 20:1-18

20  Tsopano Pasuri, mwana wa Imeri, wansembe, amenenso anali mtumiki wamkulu panyumba ya Yehova,+ anakhala tcheru kumvetsera pamene Yeremiya anali kulosera mwa kunena mawu amenewa.  Kenako Pasuri anamenya mneneri Yeremiya+ ndi kumuika m’matangadza amene anali pa Chipata Chakumtunda cha Benjamini, cha m’nyumba ya Yehova.  Ndiyeno pa tsiku lotsatira, Pasuri anamasula Yeremiya m’matangadzawo.+ Pamenepo Yeremiya anamuuza kuti: “Yehova wanena kuti dzina lako+ silikhalanso Pasuri koma Chochititsa Mantha paliponse.+  Pakuti Yehova wanena kuti, ‘Inetu ndikukusandutsa chinthu chochititsa mantha kwa iwe mwini ndi kwa anzako onse, ndipo adzaphedwa ndi lupanga la adani awo+ iwe ukuona. Anthu onse a mu Yuda ndidzawapereka m’manja mwa mfumu ya ku Babulo. Ena adzapita nawo ku Babulo ndipo ena adzawapha ndi lupanga.+  Ndipo ndidzatenga zinthu zonse zosungidwa mumzindawu, katundu wawo yense, zinthu zonse zamtengo wapatali ndi chuma chonse cha mafumu a Yuda, n’kuzipereka m’manja mwa adani awo. Ndipo adaniwo adzafunkha zinthu zimenezi ndi kupita nazo ku Babulo.  Koma kunena za iwe Pasuri, ndi onse okhala m’nyumba yako, mudzapita ku ukapolo.+ Iwe udzapita ku Babulo ndipo udzafera kumeneko ndi kuikidwa m’manda komweko pamodzi ndi anzako onse,+ chifukwa walosera kwa iwo monama.’”+  Mwandidabwitsa inu Yehova, ndipo ndadabwa. Mwagwiritsa ntchito mphamvu zanu pa ine ndipo mwapambana.+ Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse. Aliyense akungondinyoza.+  Nthawi zonse ndikalankhula mawu anu ndimalira. Ndimanena za chiwawa ndi kufunkhidwa,+ pakuti mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kutonzedwa tsiku lonse.  Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.” Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.+ 10  Pakuti ndinamva zoipa zimene ambiri anali kunena.+ Zinali zochititsa mantha paliponse. Iwo anali kunena kuti, “Fotokozani kuti ifenso tinene za iye.” Munthu aliyense anali kundiuza kuti “Mtendere!” koma anali kundiyang’anira kuti ndilakwitse chinachake+ ndipo anali kunena kuti: “Achita chinachake chopusa+ ameneyu ndipo timugonjetsa ndi kumubwezera.” 11  Koma Yehova anali nane+ ngati msilikali wamphamvu ndi woopsa.+ N’chifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana. Adzachita manyazi kwambiri chifukwa adzaona kuti sizinawayendere bwino. Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+ 12  Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama.+ Mumaona impso ndi mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+ pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+ 13  Imbirani Yehova anthu inu! Tamandani Yehova! Pakuti walanditsa moyo wa munthu wosauka m’manja mwa anthu ochita zoipa.+ 14  Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene mayi anga anandibereka lisadalitsike!+ 15  Atembereredwe munthu amene anabweretsa uthenga wabwino kwa bambo anga powauza kuti: “Mkazi wako wakuberekera mwana wamwamuna.” Munthuyo anawasangalatsa kwambiri bambo anga.+ 16  Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova waigonjetsa popanda kuimvera chisoni. M’mawa kwambiri azimva kulira kofuula ndipo masana azimva chizindikiro chochenjeza.+ 17  N’chifukwa chiyani sanandiphe ndili m’mimba kuti mayi anga akhale manda anga, ndiponso kuti akhale ndi pakati mpaka kalekale?+ 18  N’chifukwa chiyani ndinabadwa?+ Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni,+ ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?+

Mawu a M'munsi