Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yeremiya 10:1-25

10  Anthu inu, a m’nyumba ya Isiraeli, imvani zimene Yehova wanena zokutsutsani.  Yehova wanena kuti: “Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono,+ ndipo musamaope zizindikiro zakumwamba, chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+  Miyambo ya anthu amenewa+ ndi yopanda pake, chifukwa mmisiri amagwetsa mtengo+ m’nkhalango ndi kusema fano pogwiritsa ntchito sompho.+  Akatero amakongoletsa fanolo ndi siliva komanso golide.+ Kenako amatenga nyundo ndi kukhomerera mafanowo pansi ndi misomali kuti asagwe.+  Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+  Ndithudi palibe aliyense wofanana ndi inu Yehova.+ Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu ndi lalikulu ndi lamphamvu.+  Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+  Onse pamodzi ndi opanda nzeru ndiponso opusa.+ Mtengo umangowalimbikitsa kuchita zachabechabe.+  Siliva wosulidwa kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.+ Zonsezi zimakonzedwa mwaluso, ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo. Mafanowo amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Nawonso angokhala ntchito ya amisiri aluso.+ 10  Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.+ Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu mpaka kalekale.+ Dziko lapansi lidzagwedezeka ndi mkwiyo wake,+ ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzalimbe pamene iye akuidzudzula.+ 11  Mitunduyo mukaiuze izi anthu inu: “Milungu+ imene sinapange kumwamba ndi dziko lapansi+ ndi imene idzawonongedwe padziko lapansi, pansi pa thambo.” 12  Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake,+ amene mwanzeru zake+ anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikira kwake.+ 13  Mawu ake amapangitsa madzi akumwamba kuchita mkokomo,+ ndipo amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Iye wapanganso zipata zotulukirapo mvula+ ndipo amatulutsa mphepo yamkuntho m’nkhokwe zake.+ 14  Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+ 15  Iwo ndi achabechabe, ntchito yoyenera kutonzedwa.+ Mulungu akadzatembenukira kwa iwo, adzawawononga.+ 16  Koma Mulungu wa Yakobo+ sali ngati mafanowa. Iye ndi amene anapanga china chilichonse.+ Isiraeli ndiye ndodo ya cholowa chake.+ Dzina la Mulunguyo ndi Yehova wa makamu.+ 17  Iwe mkazi wokhala m’masautso,+ sonkhanitsa ndi kunyamula katundu wako.+ 18  Yehova wanena kuti: “Tsopano nditaya kutali anthu okhala padziko lapansi,+ ndipo ndiwachititsa kuvutika mtima kuti adziwe masautso awo.”+ 19  Tsoka ine chifukwa cha kuwonongedwa kwanga!+ Chilonda changa cha mkwapulo chakhala chosachiritsika. Ndipo ndanena kuti: “Ndithudi amenewa ndi matenda anga ndipo ndidzakhalabe nawo.+ 20  Hema wanga wafunkhidwa, ndipo zingwe zanga zonse zomangira hemayo aziduladula.+ Ana anga aamuna achoka ndi kundisiya ndipo kulibenso.+ Komanso palibe wotambasula kapena kudzutsa hema wanga. 21  Abusa achita zinthu mopanda nzeru,+ ndipo sanayese n’komwe kufunafuna Yehova.+ N’chifukwa chake sanachite zinthu mozindikira, ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.”+ 22  Tamvetserani nkhani imene yamveka! Kugunda kwakukulu kukumveka kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo kudzasandutsa mizinda ya Yuda kukhala mabwinja, malo obisalamo mimbulu.+ 23  Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.+ 24  Ndikonzeni, inu Yehova. Koma mundikonze ndi chiweruzo chanu+ osati mutakwiya+ chifukwa mungandifafanize.+ 25  Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu+ amene akunyalanyazani,+ ndi pa mafuko amene sakuitana padzina lanu.+ Pakuti iwo adya Yakobo.+ Amudya ndipo akupitirizabe kumuwononga.+ Malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+

Mawu a M'munsi