Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yakobo 5:1-20

5  Tamverani tsopano inu anthu achuma.+ Lirani, fuulani chifukwa cha masautso amene akubwera kwa inu.+  Chuma chanu chawola, ndipo malaya anu akunja adyedwa ndi njenjete.*+  Golide ndi siliva wanu wadyedwa ndi dzimbiri, ndipo dzimbiri limenelo lidzakhala umboni wokutsutsani. Lidzadya mnofu wa matupi anu. Zimene mwaunjika+ m’masiku otsiriza+ zili ngati moto.+  Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke, akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.  Mwalidyerera dziko lapansi ndipo mwasangalala.+ Mwanenepetsa mitima yanu pa tsiku lokaphedwa.+  Mwaweruza ndi kupha munthu wolungama. Iye akukutsutsani.+  Choncho lezani mtima abale, kufikira kukhalapo*+ kwa Ambuye. Ganizirani mmene amachitira mlimi. Iye amayembekezerabe zipatso zofunika kwambiri zotuluka m’nthaka. Amakhala wodekha mpaka itagwa mvula yoyamba ndi mvula yomaliza.  Nanunso khalani oleza mtima.+ Limbitsani mitima yanu, chifukwa kukhalapo kwa Ambuye kwayandikira.+  Musamang’ung’udzirane abale, kuopera kuti mungaweruzidwe.+ Taonani, Woweruza waima pakhomo.+ 10  Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo+ kwa aneneri+ amene analankhula m’dzina la Yehova. 11  Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawatcha odala.+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa,+ mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.+ 12  Koma koposa zonse abale anga, lekani kulumbira, kaya motchula kumwamba kapena dziko lapansi kapena lumbiro lina lililonse. Koma tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, kuti musaweruzidwe.+ 13  Kodi pali aliyense mwa inu amene akumva zowawa? Apitirize kupemphera.+ Kodi pali wina amene akukondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.+ 14  Kodi pali wina amene akudwala pakati panu?+ Aitane akulu a mpingo,+ ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta+ m’dzina la Yehova. 15  Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo,+ ndipo Yehova adzamulimbitsa.+ Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.+ 16  Choncho muululirane machimo anu poyera ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe. Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri. 17  Eliya anali munthu monga ife tomwe,+ komabe anapemphera kuti mvula isagwe, ndipo mvula sinagwe kumeneko kwa zaka zitatu ndi miyezi 6. 18  Anapempheranso, ndipo mvula inagwa kuchokera kumwamba. Nthaka inatulutsa zipatso zake. 19  Abale anga, ngati wina mwa inu wasocheretsedwa pa choonadi wina n’kumubweza,+ 20  dziwani kuti amene wabweza wochimwa panjira yake yoipa,+ adzapulumutsa moyo wa wochimwayo ku imfa+ ndipo adzakwirira machimo ambiri.+

Mawu a M'munsi

Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Onani Zakumapeto 8.