Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Yakobo 1:1-27

1  Ine Yakobo,+ kapolo+ wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikupereka moni kwa mafuko 12+ amene ali obalalika:+  Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana,+  monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.+  Koma mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira+ ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.+  Choncho ngati wina akusowa nzeru,+ azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa,+ popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.+  Koma azipempha+ ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe,+ pakuti wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo+ ndi lowindukawinduka.  Munthu wotero asaganize kuti adzalandira kanthu kwa Yehova,+  chifukwa choti iye ndi wokayikakayika,+ wosakhazikika+ m’njira zake zonse.  Koma m’bale wonyozeka akondwere chifukwa tsopano wakwezedwa,+ 10  ndipo wachuma+ akondwere chifukwa tsopano watsitsidwa, chifukwa mofanana ndi duwa la zomera, wachumayo adzafota.+ 11  Dzuwa limatuluka ndi kutentha kwake n’kufotetsa zomera, ndipo maluwa a zomerazo amathothoka. Kukongola kwake kumatha. Momwemonso munthu wachuma adzafa akutsatira njira ya moyo wake.+ 12  Wodala ndi munthu wopirira mayesero,+ chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto* ya moyo,+ umene Yehova analonjeza onse omukonda.+ 13  Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa. 14  Koma munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. 15  Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.+ Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.+ 16  Abale anga okondedwa, musasocheretsedwe.+ 17  Mphatso iliyonse yabwino+ ndi yangwiro imachokera kumwamba,+ pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo,+ ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.+ 18  Pakuti mwa chifuniro+ chake, iye anatibala ife ndi mawu a choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira pa zolengedwa zake. 19  Abale anga okondedwa, dziwani izi: Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula,+ wosafulumira kukwiya,+ 20  chifukwa mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.+ 21  Choncho siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe lochita zoipa, lomwe ndi losafunika,+ ndipo vomerezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu,+ kuti abzalidwe mwa inu.+ 22  Komabe muzichita zimene mawu amanena, osati kungomva chabe, n’kumadzinyenga ndi maganizo onama.+ 23  Pakuti ngati munthu ali wongomva mawu, koma wosachita,+ ali ngati munthu wodziyang’anira nkhope yake pagalasi. 24  Iye amadziyang’ana koma akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani. 25  Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita. 26  Ngati munthu akudziona ngati wopembedza,+ koma salamulira lilime lake,+ ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake,+ kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.+ 27  Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”