Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Tito 3:1-15

3  Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera+ ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.+ Komanso akhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino.+  Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+  Pakuti ngakhale ife nthawi inayake tinali opanda nzeru, osamvera, osocheretsedwa, akapolo a zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana, ochita zoipa, akaduka, onyansa ndiponso achidani.+  Komatu Mpulumutsi+ wathu Mulungu, anaonetsa+ kukoma mtima+ ndi kukonda anthu.  Iye sanatero chifukwa cha ntchito+ zolungama zimene tinachita+ ayi. Koma malinga ndi chifundo+ chake, anatipulumutsa mwa kutisambitsa+ ndipo chifukwa chakuti tinasambitsidwa choncho, tinafika ku moyo+ watsopano. Komanso, anatipulumutsa potisandutsa atsopano mwa mzimu woyera.+  Iye anatikhuthulira mzimu umenewu kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,+  kuti titayesedwa olungama+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ tikhale olandira cholowa+ mogwirizana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.+  Mawu amenewa ndi oona,+ ndipo ndikufuna kuti nthawi zonse uzinena zinthu zimenezi motsindika, kuti amene akukhulupirira Mulungu nthawi zonse aziganiza za mmene angapitirizire kuchita ntchito zabwino.+ Zinthu izi n’zabwino ndi zothandiza kwa anthu.  Koma iwe pewa mafunso opusa,+ kukumba mibadwo ya makolo,+ mikangano+ ndi kulimbana pa za Chilamulo,+ chifukwa zimenezi n’zosapindulitsa ndiponso n’zachabechabe. 10  Munthu wolimbikitsa mpatuko,+ usagwirizane+ nayenso utamudzudzula koyamba ndi kachiwiri,+ 11  podziwa kuti munthu wotero wapotozedwa ndipo amadziimba mlandu chifukwa akudziwa kuti akuchimwa.+ 12  Ndikadzatuma Atema kapena Tukiko+ kwa iwe, udzachite chilichonse chotheka kuti udzandipeze ku Nikopoli, chifukwa ndaganiza zokakhala kumeneko nyengo yachisanuyi.+ 13  Zena, wodziwa Chilamulo uja, komanso Apolo, uwapatse zofunika zokwanira zapaulendo, kuti asasowe kanthu.+ 14  Koma abale athu aphunzire kugwira ntchito zabwino kuti athe kupeza zinthu zofunika,+ ndiponso kuti asakhale opanda phindu.+ 15  Onse amene ali nane akupereka moni.+ Undiperekere moni kwa anthu amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Kukoma mtima kwakukulu kukhale ndi inu nonse.+

Mawu a M'munsi