Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Tito 1:1-16

1  Ine Paulo, kapolo+ wa Mulungu ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa+ ndi Mulungu. Komanso ndine wodziwa molondola+ choonadi+ chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+  kumene kwazikidwa pa chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chomwe Mulungu amene sanganame,+ analonjeza kalekale.+  Koma mu nthawi yake, anapangitsa mawu ake kuonekera kudzera mu ulaliki umene ndinapatsidwa+ mwa lamulo la Mpulumutsi wathu,+ Mulungu.  Ndikulembera Tito, mwana wanga+ weniweni m’chikhulupiriro chimodzi chomwe tili nacho: Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wa Mulungu Atate+ ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu,+ zikhale nawe.  Ndinakusiya ku Kerete+ kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike+ akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo+ amene ndinakupatsa.  Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi+ mmodzi, wa ana okhulupirira ndi osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.+  Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera.+ Pokhala mtumiki*+ wa Mulungu, asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa,*+ wandewu,+ kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo.+  Koma akhale wochereza alendo,+ wokonda zabwino, woganiza bwino,+ wolungama, wokhulupirika,+ wodziletsa,+  wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa. 10  Pakuti pali anthu ambiri osalamulirika, olankhula zopanda pake,+ ndi opotoza maganizo a ena, makamaka amene akusungabe mdulidwe+ pakati pa anthu amenewa. 11  N’kofunika kuwatseka pakamwa, pakuti anthu amenewa, pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+ akuwonongabe mabanja athunthu+ mwa kuphunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa. 12  Wina wa iwo, amenenso ndi mneneri wawo, ananena kuti: “Akerete ndi anthu abodza nthawi zonse, zilombo zakutchire zolusa,+ ndiponso alesi osusuka.” 13  Umboni umenewu ndi woona. Chifukwa cha zimenezi, pitiriza kuwadzudzula mwamphamvu,+ kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.+ 14  Asamasamale nthano zachiyuda+ ndi malamulo a anthu+ amene asiya choonadi.+ 15  Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa+ ndi opanda chikhulupiriro+ kulibe choyera, m’malomwake maganizo awo ndi chikumbumtima+ chawo n’zoipa. 16  Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu,+ koma amamukana ndi zochita zawo+ chifukwa ndi onyansa ndi osamvera, ndipo ndi osayenerera+ ntchito iliyonse yabwino.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mtumiki woyang’anira nyumba.”
Kapena kuti, “munthu womwa mowa mwauchidakwa amene amakonda kulongolola ndi kuchita ndewu akaledzera.”