Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Oweruza 8:1-35

8  Pamenepo amuna a ku Efuraimu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi? Bwanji sunatiitane pokamenya nkhondo ndi Amidiyani?”+ Ndipo iwo anayesetsa mwamphamvu kuti achite naye mkangano.+  Chotero iye anawayankha kuti: “Kodi ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?+ Kodi zokunkha za Efuraimu+ si zabwino kwambiri kuposa mphesa zimene Abi-ezeri+ wakolola?  Kodi Mulungu sanapereke Orebi ndi Zeebi,+ akalonga a Midiyani m’manja mwanu? Ndipo ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?” Atanena mawu amenewa, mkwiyo wawo unaphwa.+  Kenako, Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja, ali otopa koma akuthamangitsabe adaniwo.  Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti+ kuti: “Chonde, patsaniko anthu amene akunditsatirawa+ mitanda yobulungira ya mkate chifukwa ndi otopa, pakuti ndikuthamangitsa Zeba+ ndi Zalimuna,+ mafumu a Midiyani.”  Koma poyankha, akalonga a ku Sukoti anati: “Tipatsirenji asilikali ako mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?”+  Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “N’chifukwa chake Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m’manja mwanga, ndithu, ndidzakukwapulani ndi mitengo yaminga ya m’chipululu komanso ndi zitsamba zaminga.”+  Choncho anapitiriza ulendo wake kuchoka kumeneko n’kupita ku Penueli.+ Atafika ku Penueli, anawapemphanso chimodzimodzi, koma amuna a kumeneko anamuyankha mofanana ndi mmene amuna a ku Sukoti anamuyankhira.  Zitatero, anauzanso amuna a ku Penueli kuti: “Ndikabwerako bwino, ndidzagwetsa nsanja yanuyi.”+ 10  Pamenepa n’kuti Zeba ndi Zalimuna+ ali ku Karikori pamodzi ndi asilikali awo okwana pafupifupi 15,000. Asilikaliwa ndi amene anatsala pa gulu lonse la asilikali a Kum’mawa,+ ndipo amene anali ataphedwa anali asilikali 120,000.+ 11  Gidiyoni anayendabe panjira ya anthu okhala m’mahema, mpaka kukafika kum’mawa kwa Noba ndi Yogebeha.+ Kumeneko anathira nkhondo msasa wa adaniwo iwo asanakonzekere.+ 12  Zeba ndi Zalimuna atathawa, iye mosazengereza anawathamangitsa mpaka kuwagwira mafumu a Midiyaniwa.+ Atatero, anachititsa gulu lawo lonse kunjenjemera ndi mantha. 13  Ndiyeno Gidiyoni mwana wa Yowasi anayamba kubwerera kuchokera kunkhondo, podzera njira yopita ku Heresi. 14  Ali m’njira, anagwira mnyamata wa ku Sukoti+ amene anam’funsa mafunso.+ Pamenepo, mnyamatayo analembera Gidiyoni mayina okwana 77 a akalonga+ ndi akulu a mzinda wa Sukoti. 15  Choncho, Gidiyoni anapita kwa amuna a mumzinda wa Sukoti ndi kuwauza kuti: “Kodi Zeba ndi Zalimuna si awa? Aja amene munandinyoza nawo ponena kuti, ‘Tipatsirenji anyamata ako otopawo mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?’”+ 16  Ndiyeno anatenga akulu a mzindawo, n’kutenganso mitengo yaminga ya m’chipululu ndi zitsamba zaminga. Atatero, anaonetsa amuna a ku Sukotiwo zoopsa.+ 17  Anagwetsanso+ nsanja ya ku Penueli+ ija, ndi kupha amuna a mumzindawo. 18  Tsopano Gidiyoni anafunsa Zeba ndi Zalimuna+ kuti: “Kodi amuna amene munapha ku Tabori+ anali otani?” Poyankha iwo anati: “Iwo anali ngati iweyo. Maonekedwe ake aliyense wa iwo anali ngati mwana wa mfumu.” 19  Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “Anali abale anga, ana a amayi anga. Pali Yehova Mulungu wamoyo, sindikanakuphani mukanawasiya amoyo.”+ 20  Ndiyeno anauza Yeteri mwana wake woyamba kuti: “Nyamuka uwaphe.” Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake chifukwa anachita mantha, pakuti anali akali wamng’ono.+ 21  Choncho Zeba ndi Zalimuna anati: “Nyamuka iweyo utiphe wekha. Munthu amakhala ndi mphamvu+ zolingana ndi msinkhu wake.” Motero Gidiyoni ananyamuka ndi kupha+ Zeba ndi Zalimuna, ndipo anatenga zokongoletsa zooneka ngati mwezi zimene zinali pakhosi la ngamila zawo. 22  Kenako amuna a Isiraeli anauza Gidiyoni kuti: “Ukhale wotilamulira wathu,+ iweyo, mwana wako ndi mdzukulu wako, chifukwa watipulumutsa m’manja mwa Amidiyani.”+ 23  Koma Gidiyoni anawayankha kuti: “Ineyo sindikhala wokulamulirani, ngakhalenso mwana wanga sakhala wokulamulirani.+ Yehova ndiye azikulamulirani.”+ 24  Ndipo anawauzanso kuti: “Ndikupempheni chinthu chimodzi: Aliyense wa inu andipatse ndolo* yapamphuno+ kuchokera pa zimene wafunkha.” (Ogonjetsedwawo anali ndi ndolo zapamphuno zagolide, chifukwa anali Aisimaeli.)+ 25  Pamenepo iwo anati: “Sitilephera, tipereka.” Atatero anafunyulula nsalu, ndipo aliyense anaponyapo ndolo yapamphuno kuchokera pa zimene anafunkha. 26  Kulemera kwa ndolo zapamphuno zagolide zimene anapempha, kunali masekeli* agolide 1,700, osawerengera zokongoletsa zooneka ngati mwezi,+ ndolo ndi zovala zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ zimene mafumu a Midiyani aja anali atavala, osawerengeranso mikanda imene inali pakhosi la ngamila zawo.+ 27  Ndiyeno Gidiyoni anagwiritsa ntchito golideyo popanga chovala cha efodi,+ chimene anachisonyeza kwa anthu mumzinda wakwawo wa Ofira.+ Pamenepo Isiraeli yense anayamba kuchilambira ngati fano,*+ moti chinakhala msampha kwa Gidiyoni ndi nyumba yake.+ 28  Choncho, Amidiyani+ anagonjetsedwa ndi ana a Isiraeli, ndipo Amidiyani sanakwezenso mutu wawo. Zitatero, dziko linakhala pa mtendere zaka 40 m’masiku a Gidiyoni.+ 29  Ndipo Yerubaala,*+ mwana wa Yowasi, anabwerera kwawo ndipo anapitirizabe kukhala kunyumba kwake. 30  Gidiyoni anakhala ndi ana 70+ otuluka m’chiuno mwake, chifukwa anadzakhala ndi akazi ambiri. 31  Nayenso mdzakazi* wake wa ku Sekemu, anamubalira mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lakuti Abimeleki.+ 32  M’kupita kwa nthawi, Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali, ndipo anamuika m’manda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+ 33  Ndiyeno zinachitika kuti Gidiyoni atangomwalira, ana a Isiraeli anayambanso kupembedza Abaala,+ moti anaika Baala-beriti* kukhala mulungu wawo.+ 34  Ana a Isiraeliwo sanakumbukire Yehova Mulungu wawo,+ amene anawalanditsa m’manja mwa adani awo onse owazungulira,+ 35  ndipo sanasonyeze kukoma mtima kosatha+ kwa anthu a m’nyumba ya Yerubaala, kapena kuti Gidiyoni, pa zabwino zonse zimene iye anachitira Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masikiyo.”
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Mawu ake enieni, “anayamba kuchita nacho chiwerewere.”
Ameneyu ndi Gidiyoni. Onani Owe 6:32.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Dzinali limatanthauza, “Mwini Pangano,” kapena “Baala wa Pangano.”