Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Oweruza 2:1-23

2  Ndiyeno mngelo wa Yehova+ ananyamuka ku Giligala+ kupita ku Bokimu,+ ndipo anati: “Ndinakutulutsani mu Iguputo ndi kukulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu.+ Komanso ndinakuuzani kuti, ‘Sindidzaphwanya konse pangano langa ndi inu.+  Ndipo inu musachite pangano ndi anthu okhala m’dziko ili,+ m’malomwake mugwetse maguwa awo ansembe.’+ Koma inu simunamvere mawu anga.+ N’chifukwa chiyani mwachita zimenezi?+  Choncho nanenso ndikuti, ‘Sindiwapitikitsa pamaso panu, koma akhala msampha kwa inu,+ ndipo milungu yawo ikhala ngati nyambo.’”+  Mngelo wa Yehova atalankhula mawu amenewa kwa ana onse a Isiraeli, anthuwo anayamba kulira mokweza mawu.+  Choncho anatcha malowo dzina lakuti Bokimu.* Ndipo anapereka nsembe kwa Yehova pamalowo.  Yoswa atauza anthuwo kuti apite, aliyense wa ana a Isiraeliwo anapita ku cholowa chake, kukatenga dzikolo kukhala lawo.+  Ndipo anthuwo anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhala ndi moyo Yoswa atamwalira, akulu amene anaona ntchito zonse zazikulu zimene Yehova anachitira Isiraeli.+  Yoswa mtumiki wa Yehova, mwana wa Nuni, anamwalira ali ndi zaka 110.+  Ndipo anamuika m’manda ku Timinati-heresi,*+ m’dera limene analandira monga cholowa chake, m’dera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.+ 10  Anthu onse a m’badwo umenewo anamwalira ndi kugona ndi makolo awo,+ ndipo pambuyo pawo panauka m’badwo wina umene sunadziwe Yehova kapena ntchito zimene iye anachitira Isiraeli.+ 11  Ndiyeno ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova,+ n’kuyamba kutumikira Abaala.+ 12  Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa m’dziko la Iguputo,+ n’kuyamba kutsatira milungu ina mwa milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milungu imeneyo, moti anakhumudwitsa Yehova.+ 13  Anasiya Yehova ndi kuyamba kutumikira Baala ndi zifaniziro za Asitoreti.+ 14  Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Isiraeli,+ moti anawapereka m’manja mwa ofunkha, ndipo anayamba kufunkha zinthu zawo.+ Iye anawagulitsa kwa adani awo owazungulira+ moti sanathe kuima pamaso pa adani awo.+ 15  Kulikonse kumene apita, dzanja la Yehova linali kuwaukira ndi kuwadzetsera masoka,+ monga mmene Yehova ananenera ndiponso monga mmene Yehova analumbirira kwa iwo,+ moti iwo anali kuvutika kwambiri.+ 16  Zikatero, Yehova anali kuwapatsa oweruza,+ ndipo anali kuwapulumutsa m’manja mwa ofunkha.+ 17  Ana a Isiraeli sanamvere ngakhale oweruza awo, koma anachita chiwerewere+ ndi milungu ina+ ndi kuigwadira. Iwo anapatuka mwamsanga panjira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo anayenda m’njira imeneyo mwa kumvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite mofanana ndi makolo awo. 18  Yehova akawapatsa oweruza,+ Yehova anali kukhaladi ndi aliyense wa oweruzawo, ndipo iye anali kuwapulumutsa m’manja mwa adani awo masiku onse a moyo wa woweruzayo. Yehova anali kuchita zimenezo pakuti anali kuwamvera chisoni+ akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.+ 19  Ndiyeno zinali kuchitika kuti woweruza akamwalira, ana a Isiraeli anali kupatuka ndi kuchita zinthu zowawonongetsa kuposanso makolo awo. Anali kuchita zimenezi mwa kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Iwo sanasiye zochita zawozo ndiponso khalidwe lawo la unkhutukumve.+ 20  Chotero mkwiyo wa Yehova unayakira+ Isiraeli ndipo anati: “Popeza mtundu umenewu waphwanya pangano langa+ limene ndinalamula makolo awo kuti alisunge, ndipo sanamvere mawu anga,+ 21  ine sindipitikitsanso pamaso pawo mtundu uliwonse pa mitundu imene Yoswa anaisiya pamene ankamwalira.+ 22  Ndichita zimenezi kuti ndiyese+ Isiraeli kudzera mwa mitundu imeneyi, kuti ndione ngati angasunge njira ya Yehova mwa kuyendamo monga mmene makolo awo anachitira, kapena ayi.” 23  Choncho, Yehova analola mitundu imeneyi kukhalabe, osaipitikitsa mwamsanga,+ ndipo sanaipereke m’manja mwa Yoswa.

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Olira.”
Kapena kuti, “Timinati-sera.”