Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Oweruza 10:1-18

10  Pambuyo pa Abimeleki, panabwera Tola, munthu wa fuko la Isakara, amene anapulumutsa+ Isiraeli. Iye anali kukhala ku Samiri m’dera lamapiri la Efuraimu,+ ndipo anali mwana wa Puwa, amene anali mwana wa Dodo.  Iye anaweruza Isiraeli zaka 23. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa ku Samiri.  Pambuyo pa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi.+ Iye anaweruza Isiraeli zaka 22.  Iye anadzakhala ndi ana 30 aamuna amene anali kuyenda pa abulu 30,+ ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mizinda imeneyi ikutchedwabe kuti Havoti-yairi*+ kufikira lero, ndipo ili m’dziko la Giliyadi.  Kenako Yairi anamwalira ndipo anaikidwa ku Kamoni.  Zitatero, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ zifaniziro za Asitoreti,+ milungu ya ku Siriya,+ milungu ya ku Sidoni,+ milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya ana a Amoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Motero iwo anasiya Yehova ndipo sanam’tumikire.+  Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Isiraeli,+ moti anawagulitsa+ kwa Afilisiti+ ndi kwa ana a Amoni.+  Choncho, amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri ana a Isiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza ana onse a Isiraeli amene anali kum’mawa kwa Yorodano, m’dziko la Aamori limene linali ku Giliyadi.  Ndipo ana a Amoni anali kuwoloka Yorodano kukamenyana ndi fuko la Yuda, la Benjamini, ndi la Efuraimu, moti Isiraeli anasautsika kwambiri.+ 10  Pamenepo ana a Isiraeli anayamba kufuulira Yehova kuti awathandize.+ Iwo anati: “Takuchimwirani+ inu Mulungu wathu, chifukwa takusiyani ndipo tikutumikira Abaala.”+ 11  Ndiyeno Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Kodi Aiguputo,+ Aamori,+ ana a Amoni,+ Afilisiti,+ 12  Asidoni,+ Aamaleki+ ndi Amidiyani+ atakuponderezani,+ sindinakupulumutseni m’manja mwawo mutafuulira kwa ine? 13  Koma inu munandisiya+ n’kuyamba kutumikira milungu ina.+ N’chifukwa chake sindidzakupulumutsaninso.+ 14  Pitani, kapempheni thandizo kwa milungu+ imene mwasankhayo.+ Milungu imeneyo ndi imene ikupulumutseni pa nthawi ya nsautso yanu.” 15  Poyankha, ana a Isiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa.+ Inuyo mutichite zilizonse zimene zingakukomereni m’maso mwanu.+ Koma chonde, ingotipulumutsani lero.”+ 16  Atatero, iwo anayamba kuchotsa milungu yonse yachilendo pakati pawo+ n’kuyamba kutumikira Yehova,+ moti mtima wake+ unagwidwa ndi chisoni chifukwa cha kuvutika kwa ana a Isiraeli.+ 17  Patapita nthawi, ana a Amoni+ anasonkhanitsidwa pamodzi ndipo anamanga msasa wawo ku Giliyadi.+ Zitatero, ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi ndi kumanga msasa wawo ku Mizipa.+ 18  Ndiyeno anthu ndi akalonga a Giliyadi anayamba kufunsana kuti: “Ndani atitsogolere kukamenyana ndi ana a Amoni?+ Ameneyo akhale mtsogoleri wa anthu onse okhala m’Giliyadi.”+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Midzi ya Mahema ya Yairi.”