Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Oweruza 1:1-36

1  Ndiyeno zinachitika kuti Yoswa atamwalira,+ ana a Isiraeli anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Ndani wa ife adzayamba kupita kwa Akanani kukamenyana nawo?”  Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Fuko la Yuda ndilo lidzayamba kupita.+ Ndipo ndidzaperekadi dzikolo m’manja mwawo.”  Ndiyeno a fuko la Yuda anauza abale awo a fuko la Simiyoni kuti: “Tiyeni tipitire limodzi m’gawo la fuko lathu+ kuti tikamenyane ndi Akanani. Kenako ifenso tidzapita nanu kugawo lanu.”+ Choncho fuko la Simiyoni linapita nawo.+  Pamenepo fuko la Yuda linakwezeka mtunda, ndipo Yehova anapereka Akanani ndi Aperezi m’manja mwawo,+ mwakuti anagonjetsa amuna 10,000 ku Bezeki.  Atapeza Adoni-bezeki ku Bezeki anamenyana naye mpaka kugonjetsa Akanani+ ndi Aperezi.+  Pamenepo Adoni-bezeki anathawa, ndipo anam’thamangitsa ndi kum’gwira. Atam’gwira, anam’dula zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi.  Zitatero, Adoni-bezeki anati: “Panali mafumu 70 odulidwa zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi, amene anali kutola chakudya pansi pa tebulo langa. Mulungu wandibwezera zimene ndinachita.”+ Kenako anam’tengera ku Yerusalemu+ kumene anakafera.  Ndiyeno ana a Yuda anapitiriza kumenyana ndi mzinda wa Yerusalemu+ n’kuulanda. Anapha anthu okhala mmenemo ndi lupanga, ndipo mzindawo anautentha ndi moto.  Kenako ana a Yuda anatsika kukamenyana ndi Akanani okhala m’dera lamapiri, ku Negebu+ ndi ku Sefela.+ 10  Motero fuko la Yuda linapita kukamenyana ndi Akanani amene anali kukhala ku Heburoni,+ (poyamba dzina la mzinda wa Heburoni linali Kiriyati-ariba).+ Iwo anapha Sesai, Ahimani ndi Talimai.+ 11  Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.)+ 12  Pamenepo Kalebe+ anati: “Ndithudi, aliyense amene amenyane ndi mzinda wa Kiriyati-seferi ndi kuulanda, ndim’patsa Akisa+ mwana wanga kuti akhale mkazi wake.”+ 13  Ndipo Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe, analanda mzindawo.+ Choncho, Kalebe anam’patsa Akisa mwana wake kuti akhale mkazi wake.+ 14  Ndiyeno zinachitika kuti pamene Akisa anali kupita kunyumba, anali kulimbikitsa Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anawomba m’manja ali pabulu.*+ Atatero, Kalebe anamufunsa kuti: “Ukufuna chiyani?” 15  Ndipo iye anati: “Ndidalitseni,+ pakuti mwandipatsa malo akum’mwera, ndipo mundipatse Guloti-maimu.”* Pamenepo Kalebe anam’patsa Guloti Wakumtunda+ ndi Guloti Wakumunsi. 16  Ndiyeno ana a munthu wa mtundu wachikeni,+ amene anali apongozi ake a Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi ana a Yuda kukalowa m’chipululu cha Yuda, chimene chili kum’mwera kwa Aradi.+ Motero iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+ 17  Koma a fuko la Yuda anayendabe ndi abale awo a fuko la Simiyoni, ndipo anapha Akanani okhala ku Zefati ndi kuwononga mzindawo.+ N’chifukwa chake mzindawo unatchedwa Horima.*+ 18  Kenako fuko la Yuda linalanda Gaza+ ndi madera ake, Asikeloni+ ndi madera ake ndiponso Ekironi+ ndi madera ake. 19  Yehova anakhalabe ndi fuko la Yuda, moti linalanda dera lamapiri, koma silinathe kupitikitsa anthu okhala m’chigwa, chifukwa chakuti anthuwo anali ndi magaleta*+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.+ 20  Atapereka Heburoni kwa Kalebe monga mmene Mose analonjezera,+ Kalebe anapitikitsa ana atatu aamuna a Anaki amene anali kukhala mmenemo.+ 21  Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+ 22  Pa nthawi imeneyi, nawonso a nyumba ya Yosefe+ anapita kukamenyana ndi mzinda wa Beteli,+ ndipo Yehova anali nawo.+ 23  Pamenepo a nyumba ya Yosefe anayamba kuchita ukazitape+ pamzinda wa Beteli (poyamba dzina la mzindawu linali Luzi).+ 24  Ndiyeno azondi anaona mwamuna wina akutuluka mumzindawo, ndipo anamuuza kuti: “Tiuze mmene tingalowere mumzinda, ndipo tikukomera mtima.”+ 25  Iye anawauzadi mmene angalowere mumzindawo, ndipo iwo anapha anthu a mumzindawo ndi lupanga,+ koma anasiya mwamunayo ndi banja lake lonse ali amoyo.+ 26  Zitatero mwamunayo anapita kudziko la Ahiti+ ndi kumanga mzinda, n’kuutcha dzina lakuti Luzi. Limenelo ndilo dzina la mzindawo kufikira lero. 27  Manase+ sanatenge mzinda wa Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, ndipo sanapitikitse anthu okhala mumzinda wa Dori+ ndi midzi yake yozungulira, anthu a mumzinda wa Ibuleamu+ ndi midzi yake yozungulira, ndi anthu okhala mumzinda wa Megido+ ndi midzi yake yozungulira. Akananiwo anakakamirabe kukhala m’dziko limeneli.+ 28  Ndiyeno zinachitika kuti Aisiraeli anakhala amphamvu,+ ndipo anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanawachotseretu onse m’dzikolo.+ 29  Fuko la Efuraimu nalonso silinapitikitse Akanani amene anali kukhala ku Gezeri, moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo ku Gezeriko.+ 30  Fuko la Zebuloni+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Kitironi ndi mzinda wa Nahaloli,+ moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo+ ndipo a fuko la Zebuloni anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo.+ 31  Fuko la Aseri+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Ako ndi anthu okhala m’mizinda ya Sidoni,+ Alabu, Akizibu,+ Heliba, Afiki+ ndi Rehobu.+ 32  Choncho Aaseri anapitirizabe kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo, chifukwa chakuti sanawapitikitse.+ 33  Fuko la Nafitali+ silinapitikitse anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati,+ koma iwo anapitiriza kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo.+ Ndipo fuko la Nafitali linayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati.+ 34  Pamenepo Aamori anapitirizabe kupanikizira ana a Dani+ kudera lamapiri, ndipo sanawalole kutsikira m’chigwa.+ 35  Choncho Aamori anakakamirabe kukhala m’phiri la Herese ndi m’mizinda ya Aijaloni+ ndi Saalibimu.+ Koma dzanja la nyumba ya Yosefe linakhala lamphamvu kwambiri, moti anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Aamoriwo.+ 36  Dera la Aamori linali kuyambira kuchitunda cha Akirabimu,+ komanso ku Sela kupita chakumtunda.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Kenako anatsetsereka (anatsika) pabulupo.”
Dzinali limatanthauza, “Dera la Madzi.”
Onani mawu a m’munsi pa Nu 21:3.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.