Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Obadiya 1:1-21

 Tsopano awa ndiwo masomphenya a Obadiya: Zimene Yehova Ambuye Wamkulu Koposa wanena zokhudza Edomu ndi izi:+ “Ife tamva uthenga wochokera kwa Yehova ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti: ‘Nyamukani anthu inu, tiyeni timuukire ndi kumenyana naye.’”+  “Taona! Ndakuchepetsa pakati pa mitundu ina,+ ndipo ndakupeputsa kwambiri.+  Mtima wako wodzikuza wakunyenga,+ iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe+ pamwamba pa phiri. Iwe ukunena mumtima mwako kuti, ‘Ndani angandigwetsere pansi?’  Ngakhale malo ako atakhala pamwamba ngati a chiwombankhanga, kapena ngakhale utamanga chisa chako pakati pa nyenyezi, ine ndidzakugwetsa kuchokera pamenepo,”+ watero Yehova.  “Kodi akuba atabwera kwa iwe, kapena olanda zinthu atabwera kwa iwe usiku, angasakaze kufikira pati?+ Kodi sakhoza kungoba zimene akufuna? Kapena kodi okolola mphesa atabwera kwa iwe, sangasiyeko zina zoti munthu angathe kukunkha?+  Taonani! Mbadwa za Esau azifufuza paliponse.+ Chuma chake chobisika achifunafuna.  Anthu onse amene unachita nawo pangano akupusitsa+ ndipo akuthamangitsira kumalire. Anthu amene unali kukhala nawo mwamtendere akugonjetsa.+ Anthu amene ukudya nawo limodzi adzakutchera ukonde, ndipo udzakhala ngati munthu wosazindikira.+  Kodi pa tsiku limenelo sindidzawononga anthu anzeru mu Edomu?”+ watero Yehova. “Ndiponso kodi sindidzawononga anthu ozindikira a m’dera lamapiri la Esau?  Iwe Temani,+ anthu ako amphamvu adzachita mantha,+ chifukwa chakuti aliyense wa iwo adzaphedwa+ ndi kuchotsedwa m’dera lamapiri la Esau.+ 10  Chifukwa chakuti m’bale wako Yakobo unam’chitira zachiwawa,+ manyazi adzakugwira.+ Iwe udzawonongedwa ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.*+ 11  Pa tsiku limene unangoima n’kumaonerera, pa tsiku limene alendo anagwira gulu la asilikali la m’bale wako n’kupita nalo kudziko lina,+ ndiponso pamene alendo enieni analowa pazipata za mzinda wake+ n’kuchita maere pa Yerusalemu,+ iwe unali ngati mmodzi wa adani akewo. 12  “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka.+ Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.+ Sunayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene iwo anamva zowawa. 13  Iwe sunayenera kulowa pachipata cha anthu anga pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+ Ndithu iweyo sunayenera kuyang’anitsitsa tsoka la m’bale wako pa tsiku limene anawonongedwa. Ndipo sunayeneranso kutambasula dzanja lako ndi kutenga chuma chake pa tsiku limene iye anakumana ndi tsoka.+ 14  Iwe sunayenera kuima pamphambano kuti uzipha anthu ake amene anali kuthawa.+ Sunayenera kugwira anthu ake opulumuka ndi kuwapereka kwa adani awo pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+ 15  Tsiku la Yehova limene adzawononge mitundu yonse ya anthu lili pafupi.+ Iwe adzakuchitira zofanana ndi zimene wachitira m’bale wako.+ Zimene unachita zidzabwerera pamutu pako.+ 16  Pakuti mmene anthu inu munali kumwera vinyo paphiri langa loyera, ndi mmenenso mitundu ina yonse ya anthu izidzamwera mkwiyo wanga ngati vinyo nthawi zonse.+ Iwo adzamwa ndi kugugudiza mkwiyo wanga, ndipo zidzakhala ngati iwo kunalibe. 17  “Anthu onse opulumuka adzakhala m’phiri la Ziyoni+ ndipo phiri limeneli lidzakhala loyera.+ A nyumba ya Yakobo adzatenga zinthu zoyeneradi kukhala zawo.+ 18  Nyumba ya Yakobo idzakhala ngati moto,+ nyumba ya Yosefe idzakhala ngati malawi a moto ndipo nyumba ya Esau idzakhala ngati mapesi.+ Motowo udzayatsa mapesiwo ndi kuwanyeketsa. Sipadzakhala wopulumuka aliyense wa nyumba ya Esau,+ pakuti Yehova mwiniyo wanena. 19  Iwo adzatenga dera la Negebu kukhala lawo, komanso adzatenga dera lamapiri la Esau,+ dera la Sefela ndi dera la Afilisiti.+ Iwo adzatenganso madera a Efuraimu+ ndi Samariya kukhala awo.+ Benjamini adzatenga dera la Giliyadi+ kukhala lake. 20  Anthu amene anatengedwa kupita kudziko lina kuchokera pachiunda ichi chomenyerapo nkhondo,+ amene ndi ana a Isiraeli, adzatenga zinthu zimene zinali za Akanani+ mpaka kukafika ku Zarefati.+ Anthu amene anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu kupita kudziko lina, amene anali ku Sefaradi, adzatenga mizinda ya Negebu kukhala yawo.+ 21  “Opulumutsa+ adzabweradi paphiri la Ziyoni+ kuti adzaweruze dera lamapiri la Esau.+ Ndipo ufumu udzakhala wa Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.