Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Nyimbo ya Solomo 1:1-17

1  Nyimbo yokoma kwambiri,+ nyimbo ya Solomo:+  “Undipsompsone ndi milomo yako,+ chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo kukoma kwake.+  Mafuta+ ako odzola ndi onunkhira bwino. Dzina lako lili ngati mafuta othira pamutu.+ N’chifukwa chake atsikana amakukonda.  Nditenge,+ tiye tithawe! Chifukwatu mfumu yandipititsa m’zipinda zake zamkati.+ Tiye tikondwere ndi kusangalalira limodzi. Tiye tinene za chikondi chimene umandisonyeza osati za vinyo.+ M’pake kuti atsikana amakukonda.+  “Inu ana aakazi a ku Yerusalemu,+ ine ndine mtsikana wakuda ngati mahema a ku Kedara,+ koma wokongola ngati nsalu za mahema+ a Solomo.  Musandiyang’anitsitse chifukwa chakuti ndada, ndi dzuwatu landidetsali. Pakuti ana aamuna a mayi anga anandikwiyira. Choncho anandiika kuti ndiziyang’anira minda ya mpesa moti sindinathe kuyang’anira munda wangawanga wa mpesa.+  “Iwe amene mtima wanga umakukonda,+ tandiuza kumene umakadyetsera ziweto,+ kumene umakagonetsa ziweto masana. Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu ya namalira pakati pa magulu a ziweto za anzako?”  “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,+ tsatira mapazi a ziweto ndipo ukadyetse ana ako a mbuzi pafupi ndi mahema a abusa.”  “Kwa ine, wokondedwa wangawe+ ndiwe wokongola ngati hatchi* yaikazi ya pamagaleta* a Farao.+ 10  Masaya ako ndi okongola pakati pa tsitsi lako lomanga, ndipo khosi lako lovala mkandalo limaoneka bwino.+ 11  Ife tikupangira zokongoletsa zoti uzivala kumutu. Zokongoletsazo zikhala zozungulira, zagolide,+ zokhala ndi mikanda yasiliva.” 12  “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira, fungo labwino la nado*+ wanga likumveka kwa wokondedwa wanga.+ 13  Wachikondi wanga ali ngati kathumba ka mule*+ kwa ine. Iye adzakhala pakati pa mabere anga+ usiku wonse. 14  Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati duwa lofiirira+ m’minda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+ 15  “Ndiwe wokongola kwabasi, wokondedwa wanga.+ Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+ 16  “Iwenso ndiwe wokongola,+ wachikondi wanga. Ndiwe mnyamata wosangalatsa kwambiri. Bedi+ lathunso ndi la masamba ofewa. 17  Nyumba yathu yokongola inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,+ ndipo kudenga* kwake kuli mitengo yofanana ndi mkungudza.

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi,” kapena “kavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Chimenechi ndi chitsamba chinachake chonunkhira bwino.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “tsindwi.”