Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 9:1-23

9  M’mwezi woyamba*+ wa chaka chachiwiri, ana a Isiraeli atatuluka m’dziko la Iguputo, Yehova analankhula ndi Mose m’chipululu cha Sinai. Iye anati:  “Tsopano ana a Isiraeli akonze nsembe ya pasika+ pa nthawi yake yoikidwiratu.+  Mukonze nsembeyo pa tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo kuli kachisisira,*+ ndiyo nthawi yake yoikidwiratu. Muikonze malinga ndi malamulo ake onse, ndiponso motsatira njira zonse za kakonzedwe kake.”+  Pamenepo Mose analankhula kwa ana a Isiraeli kuti akonze nsembe ya pasika.  Iwo anakonza nsembe ya pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, madzulo kuli kachisisira, m’chipululu cha Sinai. Ana a Isiraeliwo anachita zonse malinga ndi zimene Yehova analamula Mose.+  Tsopano panali amuna ena amene anadzidetsa pokhudza mtembo wa munthu,+ moti sanathe kukonza nsembe ya pasika pa tsikulo. Chotero anakaonekera kwa Mose ndi Aroni pa tsikulo.+  Ndipo iwo ananena kuti: “Ife ndife odetsedwa chifukwa takhudza mtembo wa munthu. Ngakhale kuti zili choncho, kodi tiyeneradi kuletsedwa kupereka nsembe+ kwa Yehova pakati pa ana a Isiraeli pa nthawi yake yoikidwiratu?”  Pamenepo Mose anawayankha kuti: “Dikirani pomwepo, ndimve zimene Yehova ati alamule zokhudza inu.”+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 10  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu wina aliyense mwa inu kapena mwa mbadwa zanu, amene wadetsedwa pokhudza mtembo wa munthu,+ kapena amene ali pa ulendo wautali, akonzebe nsembe ya pasika yopereka kwa Yehova. 11  Azikonza nsembeyo m’mwezi wachiwiri+ pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira. Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda chofufumitsa, ndiponso masamba owawa.+ 12  Pasatsaleko iliyonse yoti ifike m’mawa,+ ndipo asaphwanye fupa lake lililonse.+ Aikonze motsatira malamulo onse a pasika.+ 13  Koma ngati munthu ali wosadetsedwa, kapena sanapite pa ulendo, ndipo wanyalanyaza kukonza nsembe ya pasika, munthuyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake,+ chifukwa sanapereke nsembeyo kwa Yehova pa nthawi yake yoikidwiratu. Munthuyo adzafa chifukwa cha kuchimwa kwake.+ 14  “‘Ngati pali mlendo amene akukhala pakati panu, iyenso azikonza nsembe ya pasika yopereka kwa Yehova.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a pasika, ndiponso kakonzedwe kake ka nthawi zonse.+ Pakhale malamulo ofanana kwa nonsenu, kaya mlendo kapena mbadwa.’”+ 15  Pa tsiku lomanga chihema chopatulika,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho.+ Koma kuyambira madzulo mpaka m’mawa, moto+ unali kuoneka pamwamba pa chihema chopatulikacho. 16  Zinali kuchitika motero nthawi zonse. Mtambo unali kuima pamwamba pa chihemacho masana, ndipo usiku moto unali kuonekera pamwamba pake.+ 17  Mtambowo ukanyamuka pamwamba pa chihemacho, ana a Isiraeli anali kunyamuka nthawi yomweyo.+ Ndipo pamalo pamene mtambowo waima, m’pamene ana a Isiraeli anali kumangapo msasa.+ 18  Choncho Yehova akalamula, ana a Isiraeli anali kunyamuka, ndipo Yehova akalamula, anali kumanga msasa.+ Masiku onse amene mtambo unali pamwamba pa chihemacho, iwo anali kukhalabe pamsasapo. 19  Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihema, ana a Isiraeli ankamverabe Yehova, ndipo sankachoka pamalopo.+ 20  Nthawi zina mtambowo unali kungokhala masiku owerengeka pamwamba pa chihemapo. Yehova akalamula,+ iwo anali kukhalabe pamsasapo, ndipo Yehova akalamula, iwo anali kuchoka. 21  Nthawi zina mtambowo+ unali kukhalapo kuchokera madzulo kufika m’mawa, ndipo m’mawawo mtambowo unali kuchoka, anthuwo n’kunyamuka. Kaya mtambowo uchoke masana kapena usiku, iwonso anali kunyamuka.+ 22  Kaya mtambowo ukhale pamwamba pa chihemacho masiku awiri, mwezi, kapena masiku ambiri, ana a Isiraeli anali kukhalabe pamsasa osachoka. Koma mtambowo ukanyamuka, iwo anali kuchoka.+ 23  Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka.+ Anali kumvera Yehova potsatira malangizo a Yehova odzera kwa Mose.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.