Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 7:1-89

7  Pa tsiku limene Mose anamaliza kumanga chihema chopatulika,+ anachidzoza+ n’kuchipatula, limodzi ndi zipangizo zake zonse, komanso guwa lansembe ndi ziwiya zake zonse. Zonse anazidzoza n’kuzipatula.+  Pamenepo atsogoleri a Isiraeli,+ amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anapereka zopereka zawo.+ Anatero monga atsogoleri a mafuko awo, monganso oyang’anira anthu amene anawerengedwa aja.  Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova. Zoperekazo zinali ngolo 6 zotseka pamwamba, ndi ng’ombe 12. Zimenezi zikutanthauza kuti atsogoleri awiri anapereka ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense anapereka ng’ombe yamphongo imodzi. Zoperekazo anafika nazo pachihema chopatulika.  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti:  “Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zikhale zogwiritsa ntchito pa utumiki wa pachihema chokumanako. Uzipereke kwa Alevi, aliyense malinga ndi utumiki wake.”  Choncho Mose analandira ngolo ndi ng’ombezo, n’kuzipereka kwa Alevi.  Anapereka ngolo ziwiri ndi ng’ombe zinayi kwa ana a Gerisoni, malinga ndi utumiki wawo.+  Ana a Merari anawapatsa ngolo zinayi ndi ng’ombe 8, malinga ndi utumiki wawo+ umene anali kuchita moyang’aniridwa ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.+  Koma ana a Kohati sanawagawire zinthuzo, chifukwa utumiki wawo unali wonyamula zinthu za pamalo oyera,+ ndipo anali kuzinyamulira paphewa.+ 10  Tsopano atsogoleriwo anafika ndi zopereka zawo pamwambo wotsegulira guwa lansembe,+ pa tsiku lodzoza guwalo. Anabweretsa zopereka zawozo kuguwa lansembe. 11  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kaperekedwe ka zopereka zotsegulira guwalo kakhale kotere, pa tsiku limodzi mtsogoleri mmodzi azipereka zopereka zake.”+ 12  Amene anapereka zopereka zake pa tsiku loyamba anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda. 13  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 14  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 15  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 16  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 17  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Naasoni, mwana wa Aminadabu.+ 18  Netaneli+ mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, anapereka zopereka zake pa tsiku lachiwiri. 19  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 20  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 21  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 22  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 23  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Netaneli mwana wa Zuwara. 24  Pa tsiku lachitatu panali mtsogoleri wa ana a Zebuloni, Eliyabu+ mwana wa Heloni. 25  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu. 26  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 27  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 28  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 29  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Eliyabu mwana wa Heloni.+ 30  Pa tsiku lachinayi panali mtsogoleri wa ana a Rubeni, Elizuri+ mwana wa Sedeuri. 31  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 32  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 33  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 34  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 35  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Elizuri mwana wa Sedeuri.+ 36  Pa tsiku lachisanu panali mtsogoleri wa ana a Simiyoni, Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai. 37  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 38  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 39  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 40  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 41  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Selumiyeli mwana wa Zurisadai.+ 42  Pa tsiku la 6 panali mtsogoleri wa ana a Gadi, Eliyasafu+ mwana wa Deyueli. 43  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 44  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10 chodzaza ndi zofukiza.+ 45  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 46  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 47  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Eliyasafu mwana wa Deyueli.+ 48  Pa tsiku la 7 panali mtsogoleri wa ana a Efuraimu, Elisama+ mwana wa Amihudi. 49  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 50  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 51  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 52  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 53  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Elisama mwana wa Amihudi.+ 54  Pa tsiku la 8 panali mtsogoleri wa ana a Manase, Gamaliyeli+ mwana wa Pedazuri. 55  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 56  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 57  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 58  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 59  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.+ 60  Pa tsiku la 9 panali mtsogoleri+ wa ana a Benjamini, Abidana+ mwana wa Gidoni. 61  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 62  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 63  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 64  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 65  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Abidana mwana wa Gidoni.+ 66  Pa tsiku la 10 panali mtsogoleri wa ana a Dani, Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai. 67  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 68  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza. 69  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 70  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 71  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Ahiyezeri mwana wa Amisadai.+ 72  Pa tsiku la 11 panali mtsogoleri wa ana a Aseri, Pagiyeli+ mwana wa Okirani. 73  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 74  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 75  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 76  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 77  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Pagiyeli mwana wa Okirani.+ 78  Pa tsiku la 12 panali mtsogoleri wa ana a Nafitali, Ahira+ mwana wa Enani. 79  Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 80  Anaperekanso chikho chimodzi chagolide cholemera masekeli 10, chodzaza ndi zofukiza.+ 81  Komanso anapereka ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 82  Anaperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wa nsembe yamachimo.+ 83  Ndipo za nsembe yachiyanjano,+ iye anapereka ng’ombe ziwiri, nkhosa zisanu zamphongo, mbuzi zisanu zamphongo, ndi ana a nkhosa asanu amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Izi n’zimene anapereka Ahira mwana wa Enani.+ 84  Potsegulira guwa lansembe,+ pa tsiku limene guwalo linadzozedwa, atsogoleri+ a Isiraeli anapereka izi: Mbale zikuluzikulu zasiliva 12, mbale zolowa zasiliva+ 12, zikho zagolide 12. 85  Mbale yaikulu iliyonse yasiliva inali yolemera masekeli 130, ndipo mbale yolowa iliyonse inali yolemera masekeli 70. Siliva yense wa ziwiya zonsezi anali wolemera masekeli 2,400, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera.+ 86  Anaperekanso zikho 12 zagolide+ zodzaza ndi zofukiza. Chikho chilichonse chinali cholemera masekeli 10, malinga ndi muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Golide yense wa zikho zonsezi anali wolemera masekeli 120. 87  Nyama zonse zoperekedwa za nsembe yopsereza+ zinalipo ng’ombe 12 zamphongo, nkhosa 12 zamphongo, ndi ana a nkhosa 12 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zinaperekedwa limodzi ndi nsembe zawo zambewu.+ Atsogoleriwa anaperekanso ana a mbuzi 12 a nsembe yamachimo.+ 88  Nyama zonse zoperekedwa za nsembe yachiyanjano+ zinalipo ng’ombe 24 zamphongo, nkhosa 60 zamphongo, mbuzi 60 zamphongo, ndi ana a nkhosa 60 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinaperekedwa pamwambo+ wotsegulira guwa lansembe, pambuyo poti ladzozedwa.+ 89  Nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri.+ Mulungu anali kulankhula naye motero.

Mawu a M'munsi