Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 35:1-34

35  Yehova analankhula ndi Mose m’chipululu cha Mowabu ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano,+ kuti:  “Lamula ana a Isiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapatseko Alevi mizinda+ yokhalamo. Akaperekenso kwa Aleviwo malo onse odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+  Aleviwo azikakhala m’mizindayo, ndipo malo odyetserako ziwetowo akakhala a ziweto zawo, katundu wawo ndi nyama zawo zonse.  Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapatse Aleviwo, akakhale mikono 1,000 kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse.  Mukayeze kunja kwa mzinda, mikono 2,000 kumbali yakum’mawa, mikono 2,000 kumbali yakum’mwera, mikono 2,000 kumbali yakumadzulo, ndi mikono 2,000 kumbali yakumpoto, kuzungulira mzinda. Amenewa akakhale malo odyetserako ziweto kwa anthu a m’mizindayo.  “Mukapatse Alevi mizinda 6 yoti munthu amene wapha mnzake azikathawirako.+ Kuwonjezera pa mizindayi, mukapatse Aleviwo mizinda ina 42.  Mizinda yonse imene mukapatse Alevi ikakwane 48. Mizindayi mukawapatse limodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+  Mizinda imene mukawapatseyo ikachokere kwa ana a Isiraeli.+ Fuko limene likakhale ndi mizinda yambiri mukatengeko yambiri, ndipo fuko limene likakhale ndi mizinda yochepa mukatengeko yochepa.+ Fuko lililonse likapereke ina ya mizinda yake kwa Alevi malinga ndi cholowa chawo chimene akalandire.”  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 10  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Muwoloka Yorodano kupita kudziko la Kanani.+ 11  Mukasankhe mizinda yoyenerera kwa inu, kuti ikakhale mizinda yanu yothawirako. Munthu amene wapha mnzake mwangozi azikathawira kumeneko.+ 12  Mizindayo ikakhale kothawirako munthu wopha mnzake amene akuthawa wobwezera magazi,+ kuti amene wapha mnzakeyo asaphedwe kufikira ataima pamaso pa oweruza kuti aweruzidwe.+ 13  Ndipo mizinda imene mukaperekeyo, mizinda yothawirako 6 imeneyo, izikagwira ntchito imeneyi. 14  Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yorodano,+ ndiponso mukapereke mizinda itatu tsidya linalo, m’dziko la Kanani.+ Imeneyi ikakhala mizinda yothawirako. 15  Kwa ana a Isiraeli, kwa mlendo,+ ndi kwa munthu amene wakhaliratu pakati pawo, mizinda 6 imeneyi ikakhala kothawirako aliyense amene wapha munthu mwangozi.+ 16  “‘Ngati munthu wamenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo n’kufa, ameneyo ndi wakupha munthu.+ Ndipo wakupha munthuyo ayenera kuphedwa ndithu.+ 17  Ngati walasa mnzake ndi mwala umene ungamuphe, mnzakeyo n’kufadi, ameneyo ndi wakupha munthu. Ndipo wakupha munthuyo aphedwe ndithu. 18  Ngati wamenya mnzake ndi mtengo umene ungamuphe, mnzakeyo n’kufadi, ameneyo ndi wakupha munthu. Ndipo wakupha munthuyo aphedwe ndithu. 19  “‘Wobwezera magazi+ ndi amene ayenera kupha wakupha munthuyo. Akadzangom’peza, wobwezera magaziyo adzamuphe. 20  Ndipo ngati chifukwa chodana naye anamukankha,+ kapena ngati anamulasa ndi chinthu atamubisalira,+ mnzakeyo n’kufa, 21  kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+ 22  “‘Koma ngati wamukankha mwangozi, osati chifukwa cha chidani, kapena ngati wam’ponyera chinachake mwangozi, osati mochita kum’bisalira,+ 23  kapena ngati mosaona wamulasa ndi mwala umene ungamuphe, kapena kumugwetsera mwalawo, mnzakeyo n’kufa, koma sanali naye chidani chilichonse, kapena cholinga chofuna kumuvulaza, 24  oweruza aweruze pakati pa wopha mnzakeyo ndi woyenera kubwezera magaziyo, malinga ndi malamulo amenewa.+ 25  Oweruzawo+ alanditse wakupha munthuyo m’manja mwa wobwezera magazi, ndipo am’bwezere kumzinda wothawirako kumene anathawira. Iye ayenera kukhala mumzindamo mpaka mkulu wa ansembe amene anadzozedwa ndi mafuta opatulika+ adzamwalire. 26  “‘Koma wopha munthuyo akatuluka kunja kwa malire a mzinda wothawirako kumene anathawira, 27  wobwezera magazi+ n’kumupeza kunja kwa malire a mzinda wothawirako, n’kumupha, wobwezera magaziyo alibe mlandu wa magazi. 28  Wakupha munthuyo ayenera kukhala mumzinda wothawirako kufikira mkulu wa ansembe atamwalira.+ Pambuyo pa imfa ya mkulu wa ansembe, wakupha munthuyo ayenera kubwerera kumalo a cholowa chake. 29  Amenewa akhale malamulo anu oweruzira milandu m’mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale. 30  “‘Aliyense wopezeka kuti wapha munthu,+ atatsimikiziridwa ndi mboni,+ aphedwe. Koma umboni wa munthu mmodzi si wokwanira kuti munthu aphedwe. 31  Ndipo musalandire dipo lowombolera moyo wa munthu wakupha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa.+ Aphedwe ndithu ameneyo.+ 32  Komanso musalandire dipo loperekedwa ndi cholinga chofuna kuwombola munthu amene anathawira kumzinda wothawirako kuti abwerere kwawo mkulu wa ansembe asanamwalire. 33  “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ 34  Musaipitse dziko limene mukukhalamo, limene inenso ndikukhalamo, pakuti ine Yehova ndikukhala pakati pa ana a Isiraeli.’”+

Mawu a M'munsi