Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 34:1-29

34  Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti:  “Lamula ana a Isiraeli, uwauze kuti, ‘Pamene mukukalowa m’dziko la Kanani,+ nawa malire a dziko+ limene mudzalandire ngati cholowa chanu.+  “‘Chigawo chanu chakum’mwera chiyenera kuyambira kuchipululu cha Zini, kumalire a Edomu.+ Malire anu a kum’mwera ayenera kuchokera kumathero a Nyanja Yamchere,+ kum’mawa.  Malirewo akadutse kum’mwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, n’kuloweranso kum’mwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ n’kukafika ku Azimoni.  Ndiyeno malirewo akalowere kuchigwa* cha Iguputo+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu.+  “‘Malire anu a kumadzulo+ akatsatire gombe la Nyanja Yaikulu.  “‘Malire anu a kumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+  Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo akafike ku Hamati,+ mpaka ku Zedadi.+  Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka ku Hazara-enani.+ Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto. 10  “‘Ndiyeno mukalembe malire anu a kum’mawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu. 11  Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kum’mawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akagunde malo otsetsereka a kum’mawa kwa nyanja ya Kinereti.*+ 12  Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndilo dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’” 13  Chotero Mose anauza ana a Isiraeli kuti: “Ili ndilo dziko limene ligawidwe kwa inu mwa maere+ monga cholowa chanu. Lidzagawidwa kwa inu monga momwe Yehova analamulira kuti lipatsidwe kwa mafuko 9 ndi hafu.+ 14  Fuko la ana a Rubeni mwa mabanja a makolo awo, ndi fuko la ana a Gadi mwa mabanja a makolo awo, alandira kale cholowa chawo. Ndiponso hafu ya fuko la Manase, nawonso alandira kale cholowa chawo.+ 15  Mafuko awiri ndi hafuwo alandira kale cholowa chawo kudera la kum’mawa kwa Yorodano, moyang’anana ndi Yeriko.”+ 16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 17  “Amuna amene akakugawireni malo monga cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa mwana wa Nuni.+ 18  Musankhe mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse, kuti akathandize kugawa cholowa cha malo.+ 19  Amunawo mayina awo ndi awa: Pa fuko la Yuda,+ Kalebe mwana wa Yefune, + 20  pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi, 21  pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni, 22  pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili, 23  pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi, 24  pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana, 25  pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki, 26  pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani, 27  pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi, 28  ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.” 29  Amenewa ndiwo amuna amene Yehova analamula kuti akagawire malo ana a Isiraeli, kuti akakhale ndi malo awoawo m’dziko la Kanani.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
M’Baibulo, “nyanja ya Kinereti” imatchulidwanso ndi mayina akuti, “nyanja ya Genesarete,” “nyanja ya Galileya” komanso “nyanja ya Tiberiyo.”