Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Numeri 3:1-51

3  Nayi mbiri ya mbadwa za Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose m’phiri la Sinai.+  Ana a Aroni mayina awo anali awa: woyamba anali Nadabu, kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+  Amenewa ndiwo anali mayina a ana a Aroni. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anapatsidwa mphamvu* yotumikira monga ansembe.+  Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova pamene anapereka kwa Yehova moto wosaloleka+ m’chipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Komabe, Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo.  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+  Iwo ayenera kutumikira iye ndi kutumikiranso khamu lonse pa ntchito za pachihema chokumanako.  Azisamalira ziwiya zonse+ za pachihema chokumanako, monga gawo limodzi la ntchito za ana a Isiraeli zimene a fuko la Leviwo aziwagwirira potumikira pachihema chopatulika.+  Aleviwo uwapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera mwa ana a Isiraeli.+ 10  Uike Aroni ndi ana ake kukhala ansembe, kuti azigwira ntchito yaunsembe.+ Aliyense amene si Mlevi akayandikira malowo, aziphedwa.”+ 11  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 12  “Ine ndikutenga Alevi pakati pa ana a Isiraeli m’malo mwa ana onse oyamba kubadwa+ a ana a Isiraeli ndipo iwo akhala anga. 13  Pakuti mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ M’tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo,+ ndinadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.” 14  Yehova analankhulanso ndi Mose m’chipululu cha Sinai+ kuti: 15  “Uwerenge ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo, malinga ndi mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wamwezi umodzi kupita m’tsogolo.”+ 16  Chotero, Mose anayamba kuwawerenga potsatira mawu a Yehova, monga mmene anamulamulira. 17  Ana a Levi+ anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ 18  Ana a Gerisoni, malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Libini ndi Simeyi.+ 19  Ana a Kohati,+ malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Amuramu, Izara,+ Heburoni ndi Uziyeli. 20  Ana a Merari,+ malinga ndi mayina a mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+ Awa ndiwo anali mabanja a Alevi, potsata nyumba za makolo awo. 21  Mwa ana a Gerisoni, panali banja la Alibini+ ndi banja la Asimeyi.+ Awa ndiwo anali mabanja a Agerisoni. 22  Amene anawerengedwa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo.+ Onse owerengedwa anakwana 7,500.+ 23  Mabanja a Agerisoni anali kukhala kumbuyo kwa chihema chopatulika.+ Anali kumanga msasa wawo kumadzulo. 24  Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25  Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema chopatulikacho,+ ndi nsalu zake zophimba zosiyanasiyana,+ nsalu yake yotchinga pakhomo,+ 26  nsalu za mpanda+ wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema chopatulika, ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe za chinsalu chake,+ komanso ntchito zonse zokhudza utumikiwu. 27  Mwa ana a Kohati, panali banja la Aamuramu, banja la Aizara, banja la Aheburoni ndi banja la Auziyeli. Awa ndiwo anali mabanja a Akohati.+ 28  Amuna onse owerengedwa, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 8,600. Ntchito ya amenewa inali kutumikira pamalo oyera.+ 29  Mabanja a ana a Kohati anali kumanga msasa wawo kum’mwera kwa chihema chopatulika.+ 30  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31  Ntchito yawo+ inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ndi ziwiya+ za m’malo oyerawo zimene anali kutumikira nazo, ndiponso nsalu yotchinga,+ komanso ntchito zonse zokhudza utumikiwu. 32  Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndiye anali kuyang’anira onse otumikira pamalo oyera. 33  Mwa ana a Merari, panali banja la Amali+ ndi banja la Amusi.+ Awa ndiwo anali mabanja a Amerari.+ 34  Amuna onse owerengedwa, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 6,200.+ 35  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo anali kumanga msasa wawo kumpoto kwa chihema chopatulika.+ 36  Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema chopatulika, mipiringidzo yake,+ mizati yake,+ zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi mizati, ziwiya zonse+ ndi zina zonse zokhudza utumiki umenewu.+ 37  Iwo anali kusamaliranso nsanamira+ za mpanda wozungulira bwalo ndiponso zitsulo zokhazikapo nsanamirazo,+ komanso zikhomo ndi zingwe zake zolimbitsira nsanamirazo. 38  Amene anali kumanga msasa wawo kum’mawa kwa chihema chopatulika, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira m’malo opatulika,+ kutumikira ana a Isiraeli. Aliyense amene si Mlevi akayandikira malowo, anayenera kuphedwa.+ 39  Alevi onse amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova, malinga ndi mabanja awo, amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, analipo 22,000. 40  Kenako Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Uwerenge ana aamuna onse oyamba kubadwa a Isiraeli, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo,+ ndipo ulembe mayina awo. 41  Unditengere Alevi akhale anga m’malo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa a Isiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi m’malo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za ana a Isiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42  Monga mmene Yehova anamulamulira, Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli. 43  Ndipo ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira amwezi umodzi kupita m’tsogolo, anakwana 22,273. 44  Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti: 45  “Unditengere Alevi akhale anga m’malo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli. Unditengerenso ziweto za Alevi zikhale zanga m’malo mwa ziweto za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova. 46  Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47  utenge masekeli* asanu pa munthu aliyense.+ Utenge muyezo wa sekeli la kumalo oyera. Sekeli limodzi likukwana magera 20.+ 48  Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera ana a Isiraeli otsala poyerekezera ndi chiwerengero cha Alevi.” 49  Chotero, Mose analandira ndalama zowombolera ana a Isiraeli oyamba kubadwa otsala poyerekezera ndi ndalama za dipo la Alevi. 50  Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Isiraeli, analandira ndalama za masekeli okwanira 1,365, pamuyezo wa sekeli la kumalo oyera. 51  Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, malinga n’zimene Yehova analamula Mose.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.