Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 29:1-40

29  “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Lizikhala tsiku lanu loliza lipenga.+  Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+  Muziperekanso ufa wosalala wothira mafuta monga nsembe zake zambewu. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pang’ombe yamphongoyo, magawo awiri mwa magawo 10 pankhosa yamphongoyo,+  ndi gawo limodzi mwa magawo 10 pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7+ amenewo.  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi wamphongo, monga nsembe yamachimo yophimbira machimo anu.+  Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo malinga ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zotentha ndi moto zopereka fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+  “‘Pa tsiku la 10 la mwezi wa 7 umenewu, muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzidzisautsa.*+ Musamagwire ntchito yamtundu uliwonse.+  Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe yaing’ono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ Muzionetsetsa kuti nyamazo n’zopanda chilema.+  Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Popereka ng’ombe yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongoyo+ muziperekanso ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 10  Popereka aliyense wa ana a nkhosa 7 amphongowo,+ muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 11  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yamachimo pa tsiku lophimba machimo, ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe zake zambewu ndiponso zachakumwa.+ 12  “‘Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7,+ muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Muzichita chikondwerero kwa Yehova masiku 7.+ 13  Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembe imeneyo izikhala ya ng’ombe 13 zazing’ono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazi n’zopanda chilema.+ 14  Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Iliyonse ya ng’ombe 13 zamphongozo muziiperekera ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Iliyonse ya nkhosa zamphongo ziwirizo muziiperekera ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 15  Aliyense wa ana a nkhosa 14 amphongowo, muzim’perekera ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 16  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 17  “‘Pa tsiku lachiwiri, muzipereka ng’ombe 12 zazing’ono zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 18  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 19  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+ Muzim’pereka kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu, limodzi ndi nsembe zake zachakumwa.+ 20  “‘Pa tsiku lachitatu, muzipereka ng’ombe 11 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 21  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 22  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa. 23  “‘Pa tsiku lachinayi, muzipereka ng’ombe 10 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 24  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 25  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 26  “‘Pa tsiku lachisanu, muzipereka ng’ombe 9 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 27  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 28  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 29  “‘Pa tsiku la 6, muzipereka ng’ombe 8 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 30  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 31  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 32  “‘Pa tsiku la 7, muzipereka ng’ombe 7 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 33  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse la zimenezi.+ 34  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 35  “‘Pa tsiku la 8, muzichita msonkhano wapadera.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ 36  Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Nsembeyo izikhala ya ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, wopanda chilema.+ 37  Popereka nyama zimenezi, ng’ombe yamphongo, nkhosa yamphongo, ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu+ ndi nsembe zake zachakumwa,+ malinga ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ 38  Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo,+ kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+ 39  “‘Muzipereka zimenezi kwa Yehova pa zikondwerero zanu.+ Muzizipereka kuwonjezera pa zopereka zanu zalonjezo,+ ndi nsembe zanu zaufulu+ zimene mumapereka monga nsembe zanu zopsereza,+ nsembe zanu zambewu,+ nsembe zanu zachakumwa,+ ndi nsembe zanu zachiyanjano.’”+ 40  Pamenepo Mose anauza ana a Isiraeli zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+

Mawu a M'munsi

“Kudzisautsa” pano kungatanthauze kusala chakudya ndiponso kutsatira malamulo ena ofanana ndi kuchita zimenezi.