Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Numeri 21:1-35

21  Tsopano mfumu ya Akanani ya ku Aradi+ yomwe inali kukhala ku Negebu,+ inamva kuti Aisiraeli akubwera kudzera njira ya ku Atarimu. Itamva zimenezo inapita kukamenyana nawo ndipo Aisiraeli ena inawagwira ndi kupita nawo kudziko lake.  Aisiraeli ataona zimenezo, analonjeza kwa Yehova kuti:+ “Mukapereka anthuwa m’manja mwathu, ndithu ifenso tidzawononga mizinda yawo.”+  Yehova anamva mawu a Aisiraeli, ndipo anapereka Akananiwo m’manja mwawo. Aisiraeli anawononga Akananiwo limodzi ndi mizinda yawo. N’chifukwa chake malowo anawatcha Horima.*+  Pamene Aisiraeliwo anali pa ulendo kuchokera kuphiri la Hora+ kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira, kulambalala dziko la Edomu,+ anayamba kutopa chifukwa cha njirayo.  Choncho iwo anayamba kuwiringula kwa Mulungu+ ndiponso Mose,+ kuti: “Munatitulutsiranji m’dziko la Iguputo? Kodi mumafuna kuti tidzafere m’chipululu?+ Kuno chakudya kulibe, madzinso kulibe.+ Chakudya chonyansachi chafika potikola.”+  Pamenepo Yehova anatumiza njoka zapoizoni pakati pawo,+ ndipo zinayamba kuwaluma moti Aisiraeli ambiri anafa.+  Anthuwo ataona zimenezo, anapita kwa Mose n’kumuuza kuti: “Tachimwa ife,+ chifukwa talankhula mowiringula kwa Yehova ndiponso kwa inuyo. Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.”+ Pamenepo Mose anayamba kuwapepesera kwa Mulungu.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Upange chifanizo cha njoka yapoizoni* ndipo uchiike pamtengo wachizindikiro. Munthu aliyense amene walumidwa, akayang’ana njokayo akhalebe ndi moyo.”+  Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa+ ndi kuiika pamtengo wachizindikirowo.+ Ndipo zinachitikadi kuti munthu akalumidwa ndi njoka n’kuyang’ana+ njoka yamkuwayo, anali kukhalabe ndi moyo.+ 10  Pambuyo pake, ana a Isiraeli anasamuka n’kukamanga msasa ku Oboti.+ 11  Kenako anasamuka ku Oboti n’kukamanga msasa ku Iye-abarimu,+ m’chipululu choyang’anana ndi dziko la Mowabu, kotulukira dzuwa. 12  Atachoka kumeneko anakamanga msasa m’chigwa* cha Zeredi.+ 13  Atasamuka kumeneko anakamanga msasa m’dera la chigwa cha Arinoni,+ m’chipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori. 14  N’chifukwa chake buku la Nkhondo za Yehova limati: “Vahebi ku Sufa, ndi zigwa* za Arinoni. 15  Mitsinje ya m’zigwazo imakafika ku Ari+ ndipo imayenda m’malire a dziko la Mowabu.” 16  Atachoka kumeneko anapita ku Beere.+ Kumeneku ndi kuchitsime kumene Yehova anauza Mose kuti: “Sonkhanitsa anthuwo kuti ndiwapatse madzi.”+ 17  Pa nthawi imeneyo Aisiraeli anaimba nyimbo+ yakuti: “Tumphuka, chitsime iwe! Vomerezani nyimboyo, anthu inu! 18  Chitsimechi n’chokumbidwa ndi akalonga. Chofukula anthu olemekezeka, Chofukula ndi ndodo ya mtsogoleri wa asilikali,+ chofukula ndi ndodo zawo.” Atachoka kuchipululucho anafika ku Matana. 19  Atachoka ku Matana anafika ku Nahaliyeli, ndipo atachoka ku Nahaliyeli anafika ku Bamoti.+ 20  Atachoka ku Bamoti anafika kuchigwa cha dziko la Mowabu,+ kumalire ndi mzinda wa Pisiga.+ Chitunda cha Pisiga chinayang’anana ndi dera la Yesimoni.+ 21  Tsopano Aisiraeli anatuma amithenga kupita kwa Sihoni+ mfumu ya Aamori kukanena kuti: 22  “Tiloleni tidzere m’dziko lanu. Sitipatukira pamunda uliwonse, kapena pamunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mumsewu wa mfumu mpaka titadutsa m’dziko lanu.”+ 23  Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adzere m’dziko lake.+ M’malomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse n’kupita kukamenyana ndi Aisiraeli m’chipululumo. Anakafika ku Yahazi,+ kumene anayamba kumenyana ndi Aisiraeli. 24  Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ n’kuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi ana a Amoni, chifukwa Yazeri+ ali kumalire kwa ana a Amoni.+ 25  Choncho Aisiraeli analanda mizinda yonseyi n’kuyamba kukhala m’mizinda yonse ya Aamori+ ku Hesiboni,+ ndi m’midzi yake yonse yozungulira. 26  Anayamba kukhala kumeneko chifukwa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni.+ Sihoni inali mfumu ya Aamori,+ ndipo iye ndiye anamenyana ndi mfumu ya Mowabu m’mbuyomo, n’kulanda dziko lonse limene linali m’manja mwake mpaka kuchigwa cha Arinoni.+ 27  N’chifukwa chake olakatula ndakatulo zonyoza anali kunena kuti: “Bwerani ku Hesiboni. Mzinda wa Sihoni umangidwe n’kukhala wolimba. 28  Pakuti moto watuluka ku Hesiboni,+ lawi lamoto latuluka m’tauni ya Sihoni. Lanyeketsa Ari+ mzinda wa ku Mowabu, lanyeketsa eni ake a malo okwezeka a ku Arinoni. 29  Tsoka iwe Mowabu! Ndithu mudzafafanizika, inu anthu a Kemosi!+ Ndithudi, iye adzapangitsa ana ake aamuna kukhala othawa kwawo, ndipo adzapereka ana ake aakazi mu ukapolo kwa Sihoni, mfumu ya Aamori. 30  Choncho tiyeni tiwalase. Ndithu Hesiboni adzafafanizika mpaka ku Diboni,+ Amayi adzaphedwa mpaka ku Nofa, amuna mpaka ku Medeba.”+ 31  Tsopano Aisiraeli anayamba kukhala m’dziko la Aamori.+ 32  Pamenepo Mose anatumiza anthu ena kuti akazonde mzinda wa Yazeri.+ Atatero, Aisiraeliwo analanda midzi yozungulira mzindawo, n’kupitikitsa Aamori omwe anali kukhalamo.+ 33  Pambuyo pake, anatembenuka ndi kulowera njira ya ku Basana.+ Pamenepo, Ogi+ mfumu ya Basana inatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kukamenyana nawo pankhondo ya ku Edirei.+ 34  Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndim’pereka ndithu m’manja mwako. Ndim’pereka pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake.+ Umuchite zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anali kukhala m’Hesiboni.”+ 35  Choncho Aisiraeliwo anapha iyeyo, ana ake ndi anthu ake onse, moti sipanatsale ndi mmodzi yemwe wopulumuka,+ ndipo analanda dziko lake.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Horima” limatanthauza “chinthu choperekedwa kuti chiwonongedwe kotheratu.”
Kapena kuti “njoka yamoto.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.