Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Nehemiya 13:1-31

13  Pa tsiku limenelo buku+ la Mose linawerengedwa+ pamaso pa anthuwo. Iwo anapeza kuti m’bukumo analembamo kuti Muamoni+ ndi Mmowabu+ aliyense sayenera kubwera mumpingo wa Mulungu woona mpaka kalekale,+  chifukwa iwowa sanachingamire ana a Isiraeli kuti awapatse chakudya+ ndi madzi.+ M’malomwake, analemba ganyu Balamu+ kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+  Choncho atangomva chilamulocho,+ anayamba kupatula+ khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana kuwachotsa pakati pa Isiraeli.  Zimenezi zisanachitike, panali Eliyasibu+ wansembe amene anali kuyang’anira zipinda zodyeramo+ m’nyumba ya Mulungu wathu, ndipo anali wachibale wa Tobia.+  Eliyasibu anakonzera Tobia chipinda chachikulu chodyeramo+ m’chipinda chimene nthawi zonse anali kuikamo nsembe yambewu,+ lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda a pazipata anayenera kulandira, komanso zimene anali kupereka kwa ansembe.  Nthawi yonseyi ine sindinali mu Yerusalemu, pakuti m’chaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke.+  Ndiyeno ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinaona zoipa zimene Eliyasibu+ anachita mwa kukonzera Tobia+ chipinda m’bwalo la nyumba+ ya Mulungu woona.  Zimenezi zinandiipira kwambiri.+ Choncho, katundu yense wa m’nyumba ya Tobia ndinam’ponyera kunja+ kwa chipinda chodyeramo.  Zitatero ndinalamula kuti ayeretse+ zipinda zodyeramo+ ndipo anachitadi zomwezo. Kenako ndinabwezera pamalo pake ziwiya+ za nyumba ya Mulungu woona pamodzi ndi zopereka zambewu ndi lubani.+ 10  Ndiyeno ndinazindikira kuti magawo+ a Alevi sanali kuperekedwa kwa iwo, moti aliyense wa Aleviwo ndi oimba amene anali kutumikira anathawa ndipo anapita kumunda wake.+ 11  Zitatero ndinayamba kuimba mlandu+ atsogoleriwo+ ndi kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani nyumba ya Mulungu woona yasiyidwa chonchi?”+ Pamenepo ndinawasonkhanitsa pamodzi ndipo ndinawaika pamalo awo ogwirira ntchito. 12  Anthu onse a mu Yuda anabweretsa kumalo osungira zinthu+ chakhumi+ cha mbewu,+ cha vinyo watsopano+ ndiponso cha mafuta.+ 13  Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba ndi Pedaya mmodzi mwa Alevi, kuti akhale oyang’anira malo osungira zinthu. Amenewa anali kuyang’anira Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya,+ pakuti anthu anali kuwaona kuti ndi okhulupirika.+ Iwowa anapatsidwa udindo wogawa+ zinthu kwa abale awo. 14  Mundikumbukire,+ inu Mulungu wanga, chifukwa cha zinthu zimenezi ndipo musaiwale+ ntchito za kukoma mtima kosatha zimene ndachitira nyumba+ ya Mulungu wanga ndi onse otumikira kumeneko. 15  Masiku amenewo ku Yuda ndinaona anthu akuponda moponderamo mphesa tsiku la sabata.+ Anali kubweretsa mbewu ndi kuzikweza+ pa abulu.+ Analinso kukweza pa abuluwo vinyo, mphesa, nkhuyu+ ndi katundu wosiyanasiyana ndipo anali kubwera nazo ku Yerusalemu tsiku la sabata.+ Ine ndinawadzudzula pa tsiku limene anali kugulitsa zinthu zimenezi. 16  Anthu a ku Turo+ anali kukhala mumzindawo ndipo anali kubweretsa nsomba ndi malonda osiyanasiyana.+ Iwo anali kugulitsa zinthu zimenezi pa tsiku la sabata kwa ana a Yuda mu Yerusalemu. 17  Choncho ndinayamba kuimba mlandu anthu olemekezeka+ a ku Yuda kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita zinthu zoipa, mpaka kuipitsa tsiku la sabata? 18  Kodi izi si zimene makolo anu anachita,+ mwakuti Mulungu wathu anadzetsa tsoka lonseli+ pa ife komanso pamzinda uwu? Koma inu mukuwonjezera kuyaka kwa mkwiyo wake pa Isiraeli mwa kuipitsa sabata.”+ 19  Ndiyeno mdima utafika pazipata za Yerusalemu, sabata lisanayambe, ndinapereka lamulo ndipo zitseko zinayamba kutsekedwa.+ Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo kufikira sabata litatha. Ndipo ndinaika ena mwa atumiki anga m’zipata kuti munthu asalowe ndi katundu tsiku la sabata.+ 20  Choncho ochita malonda ndi ogulitsa zinthu zosiyanasiyana anagona panja pa Yerusalemu kawiri. 21  Pamenepo ndinawachenjeza+ kuti: “N’chifukwa chiyani mukugona kunja kwa mpanda? Mukachitanso zimenezi ndikukhaulitsani.”+ Kuyambira nthawi imeneyo sanabwerenso pa tsiku la sabata. 22  Ndiyeno ndinauza Alevi+ kuti pobwera azidziyeretsa nthawi zonse+ komanso azilondera zipata za mzinda+ kuti tsiku la sabata likhale loyera.+ Inu Mulungu wanga, mundikumbukirenso+ pa zimenezi ndipo mundimvere chifundo malinga ndi kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+ 23  Komanso ndinaona kuti Ayuda ena anali atakwatira+ akazi achiasidodi,+ achiamoni ndi achimowabu.+ 24  Hafu ya ana awo aamuna anali kulankhula Chiasidodi ndipo palibe amene ankatha kulankhula Chiyuda,+ koma anali kulankhula chinenero cha anthu ena. 25  Ndiyeno ndinayamba kuwaimba mlandu ndi kuwatemberera.+ Ena mwa amuna amenewo ndinawamenya,+ kuwazula tsitsi ndi kuwalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti:+ “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+ 26  Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli?+ Mwa mitundu yonse panalibe mfumu yofanana naye.+ Iye anakondedwa ndi Mulungu wake,+ mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi achilendo anamuchimwitsa.+ 27  Kodi si zodabwitsa kuti inunso mukuchita choipa chachikulu chimenechi, mwa kukwatira akazi achilendo, kumene ndi kuchita mosakhulupirika kwa Mulungu wanu?”+ 28  Ndiyeno mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni.+ Choncho ndinamuthamangitsa, kum’chotsa pamaso panga.+ 29  Inu Mulungu wanga, akumbukireni amenewa chifukwa anaipitsa+ unsembe ndiponso pangano+ limene munachita ndi ansembe ndi Alevi.+ 30  Ndiyeno ndinawayeretsa+ mwa kuchotsa chilichonse chachilendo. Ndinapereka ntchito kwa ansembe ndi Alevi, aliyense ndinam’patsa ntchito yake,+ 31  ngakhale ntchito yobweretsa nkhuni+ pa nthawi zoikidwiratu ndi mbewu zoyamba kucha. Inu Mulungu wanga, mundikumbukire+ pa zabwino zimene ndinachita.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.