Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Nehemiya 12:1-47

12  Otsatirawa anali ansembe ndi Alevi amene anapita ndi Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa:+ Seraya, Yeremiya, Ezara,  Amariya,+ Maluki, Hatusi,  Sekaniya, Rehumu, Meremoti,  Ido, Ginetoi, Abiya,  Miyamini, Maadiya, Biliga,  Semaya,+ Yoyaribi, Yedaya,+  Salelu,* Amoki,+ Hilikiya ndi Yedaya.+ Amenewa ndiwo anali atsogoleri a ansembe komanso a abale awo m’masiku a Yesuwa.+  Ndiyeno panali Alevi awa: Yesuwa,+ Binui,+ Kadimiyeli,+ Serebiya, Yuda ndi Mataniya.+ Mataniya ndi abale akewa anali oyang’anira oimba nyimbo zoyamika Mulungu.  Bakibukiya ndi Uni amene ndi abale awo, anaima moyang’anizana nawo kuti azigwira ntchito ya ulonda. 10  Yesuwa anabereka Yoyakimu,+ Yoyakimu anabereka Eliyasibu,+ Eliyasibu anabereka Yoyada.+ 11  Yoyada anabereka Yonatani, Yonatani anabereka Yaduwa.+ 12  M’masiku a Yoyakimu kunali ansembe awa, atsogoleri a nyumba za makolo:+ woimira nyumba ya Seraya+ anali Meraya, woimira nyumba ya Yeremiya anali Hananiya. 13  Woimira nyumba ya Ezara+ anali Mesulamu, woimira nyumba ya Amariya anali Yehohanani. 14  Woimira nyumba ya Maluka anali Yonatani, woimira nyumba ya Sebaniya+ anali Yosefe. 15  Woimira nyumba ya Harimu+ anali Adena, woimira nyumba ya Merayoti anali Helikai. 16  Woimira nyumba ya Ido anali Zekariya, woimira nyumba ya Ginetoni anali Mesulamu. 17  Woimira nyumba ya Abiya+ anali Zikiri, woimira nyumba ya Miniyamini* anali . . . ,* woimira nyumba ya Moadiya anali Pilitai. 18  Woimira nyumba ya Biliga+ anali Samuwa, woimira nyumba ya Semaya anali Yehonatani. 19  Woimira nyumba ya Yoyaribi anali Matenai, woimira nyumba ya Yedaya+ anali Uzi. 20  Woimira nyumba ya Salai anali Kalai, woimira nyumba ya Amoki anali Ebere. 21  Woimira nyumba ya Hilikiya anali Hasabiya ndipo woimira nyumba ya Yedaya+ anali Netaneli. 22  M’masiku a Eliyasibu,+ Yoyada,+ Yohanani ndi Yaduwa,+ mayina a Alevi komanso ansembe anali kuwalemba m’gulu la atsogoleri a nyumba za makolo mpaka kudzafika m’nthawi ya ufumu wa Dariyo Mperisiya. 23  Mayina a ana aamuna a Levi, monga atsogoleri a nyumba za makolo,+ analembedwa m’buku la zochitika pa nthawi imeneyo mpaka kudzafika m’masiku a Yohanani, mwana wa Eliyasibu. 24  Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya+ ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo anaima moyang’anizana nawo kuti azitamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi lamulo+ la Davide, munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda. 25  Mataniya,+ Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu+ anali kulondera monga alonda a m’zipata.+ Amenewa anali kulondera pafupi ndi zipinda zosungiramo zinthu m’zipata za kachisi. 26  Anthu amenewa anakhalapo m’masiku a Yoyakimu+ mwana wa Yesuwa+ amene anali mwana wa Yozadaki,+ komanso m’masiku a Nehemiya+ amene anali bwanamkubwa, ndi Ezara+ amene anali wansembe komanso wokopera Malemba.+ 27  Ndiyeno mwambo wotsegulira+ mpanda wa Yerusalemu uli pafupi kuchitika, anthu anafunafuna Alevi m’malo awo onse ndi kubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala ndi kuyamika+ Mulungu mwa kuimba nyimbo+ pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe+ ndi azeze.+ 28  Ana aamuna a oimbawo anasonkhana pamodzi kuchokera m’Chigawo*+ chapafupi, m’madera onse ozungulira Yerusalemu komanso m’midzi yonse kumene Anetofa anali kukhala.+ 29  Ena anachokera ku Beti-giligala+ komanso m’dera la Geba+ ndi la Azimaveti,+ pakuti kumeneko kunali midzi+ imene oimba anamanga kuzungulira Yerusalemu yense. 30  Ndiyeno ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ ndi kuyeretsanso anthu,+ zipata+ ndi khoma la mpandawo.+ 31  Kenako ine ndinabwera ndi akalonga+ a Yuda pampandawo. Komanso ndinaika magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika+ Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu limodzi la oimba linali kuyenda pampandawo kudzanja lamanja molunjika Chipata cha Milu ya Phulusa.+ 32  Hoshaya ndi hafu ya akalonga a Yuda anayamba kuyenda pambuyo pa oimbawo, 33  komanso Azariya, Ezara, Mesulamu, 34  Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. 35  Mwa ana a ansembe oimba malipenga+ panalinso Zekariya mwana wa Yonatani. Yonatani anali mwana wa Semaya, Semaya anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali mwana wa Mikaya, Mikaya anali mwana wa Zakuri,+ ndipo Zakuri anali mwana wa Asafu.+ 36  Panalinso Semaya, Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, Yuda ndi Haneni, abale ake a Zekariya. Amenewa anali ndi zipangizo+ zoimbira za Davide, munthu wa Mulungu woona, ndipo Ezara+ wokopera Malemba ndiye anali kuwatsogolera. 37  Oimbawo atafika pa Chipata cha Kukasupe,+ gulu lowatsatira lija lili pambuyo pawo, anayenda pamalo okwera a mpandawo kudutsa pa Masitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide+ mpaka kukafika kumtunda kwa Nyumba ya Davide. Kenako anafika ku Chipata cha Kumadzi,+ kum’mawa kwa chipatacho. 38  Gulu lina loimba nyimbo zoyamika+ Mulungu linali kuyenda patsogolo, ndipo ine ndinali pambuyo pawo pamodzi ndi hafu ya anthuwo. Oimbawo anayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 39  Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda. 40  Kenako magulu awiri oimba nyimbo zoyamikawo+ anafika panyumba+ ya Mulungu woona. Ine pamodzi ndi atsogoleri amene ndinali nawo tinafikanso komweko.+ 41  Kunafikanso ansembe otsatirawa okhala ndi malipenga:+ Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, Hananiya, 42  Maaseya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezeri. Ndipo oimba pamodzi ndi Izirahiya woyang’anira wawo anali kuimba mokweza.+ 43  Pa tsiku limenelo anapereka nsembe zochuluka+ ndipo anasangalala+ pakuti Mulungu woona anawachititsa kusangalala kwambiri.+ Akazi+ ndi ana+ nawonso anasangalala, mwakuti phokoso la chisangalalo cha Yerusalemu linamveka kutali.+ 44  Kuwonjezera apo, pa tsiku limenelo anaika amuna kuti aziyang’anira zipinda+ zosungiramo zinthu zosiyanasiyana,+ zopereka,+ mbewu zoyambirira+ ndi chakhumi.+ Anawapatsa udindo wosonkhanitsira m’zipindamo gawo loyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ malinga ndi chilamulo,+ kuchokera m’minda yonse ya m’mizinda yawo. Yuda anali kusangalala chifukwa ansembe ndi Alevi+ anali kuchita utumiki wawo. 45  Choncho ansembe ndi Alevi pamodzi ndi oimba+ ndi alonda a pazipata+ anayamba kusamalira udindo+ wawo kwa Mulungu ndi kusunga lamulo lakuti azikhala oyera,+ malinga ndi lamulo la Davide ndi mwana wake Solomo. 46  Kalelo m’masiku a Davide ndi Asafu, kunali atsogoleri a oimba nyimbo+ ndipo anthu anali kuimba nyimbo zotamanda ndi kuyamika Mulungu.+ 47  Aisiraeli onse m’masiku a Zerubabele+ komanso m’masiku a Nehemiya+ anali kupereka gawo loyenera kwa oimba+ ndi alonda a pachipata+ malinga ndi zofunikira zawo za tsiku ndi tsiku. Ndipo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa Alevi.+ Aleviwo anali kupatula gawolo ndi kulipereka kwa ana a Aroni.

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti ameneyu ndi Salai wotchulidwa m’vesi 20.
Mu vesi 5 akutchedwa “Miyamini.”
Zikuoneka kuti m’Malemba Achiheberi sanam’tchule dzina.
N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Yorodano.