Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Nahumu 1:1-15

1  Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi:  Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+  Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+ komatu Yehova salephera kulanga wolakwa.+ Njira yake ili mumphepo yowononga ndi mumphepo yamkuntho. Mitambo ndilo fumbi lopondapo mapazi ake.+  Amadzudzula nyanja+ ndi kuiphwetsa ndipo amaumitsa mitsinje yonse.+ Basana ndi Karimeli afota+ ndipo maluwa a mitengo ya ku Lebanoni nawonso afota.  Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+ Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+  Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+ Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye.  Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo+ pa tsiku la nsautso.+ Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+  Adzafafaniza mzinda umenewo+ ndi madzi osefukira ndipo mdima udzathamangitsa adani ake.+  Kodi anthu inu mungakonze chiwembu chotani kuti muukire Yehova?+ Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso. Sipadzakhalanso nsautso.+ 10  Ngakhale kuti iwo alukanalukana ngati minga+ ndipo aledzera ngati kuti amwa mowa,+ adzatenthedwa ngati mapesi ouma.+ 11  Mwa iwe mudzatuluka wina amene akuganiza zochitira Yehova zoipa+ ndi kulangiza anthu zinthu zopanda pake.+ 12  Yehova wanena kuti: “Ngakhale kuti iwo anali achikwanekwane ndiponso anali ndi mphamvu zambiri, adzadulidwa+ ndipo wina adzawaukira. Pamenepo ndidzakusautsa kufikira pamene sudzafunikiranso kusautsidwa.+ 13  Tsopano ndidzathyola goli lake lonyamulira katundu ndi kulichotsa pa iwe,+ ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo.+ 14  Koma ponena za iwe, Yehova walamula kuti, ‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako.+ Ndidzadula zifaniziro zosema ndi zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndipo ndidzazitaya kunja kwa nyumba za milungu yako. Ndidzakukonzera manda+ chifukwa ndiwe wopanda pake.’ 15  “Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.+ Iye akulengeza za mtendere. Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza+ chifukwa palibe munthu aliyense wopanda pake amene adzadutsa pakati pako.+ Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”+

Mawu a M'munsi