Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 7:1-29

7  Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira,+ ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.+  Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero,+ chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake.  Kuli bwino kumva chisoni kusiyana ndi kuseka,+ pakuti nkhope yachisoni imachititsa kuti mtima wa munthu ukhale wabwino.+  Mtima wa anthu anzeru umakhala m’nyumba yamaliro, koma mtima wa anthu opusa umakhala m’nyumba yachisangalalo.  Kuli bwino kumvetsera munthu wanzeru akamakudzudzula,+ kusiyana ndi kumvetsera nyimbo ya anthu opusa.+  Pakuti kuseka kwa anthu opusa+ kumamveka ngati kuthetheka kwa minga zomwe zikuyaka pansi pa mphika. Izinso n’zachabechabe.  Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mphatso ikhoza kuwononga mtima wa munthu.  Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake, ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.+  Usamafulumire kukwiya mumtima mwako,+ pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima. 10  Usanene kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?” Pakuti si nzeru+ kufunsa funso lotere. 11  Munthu wanzeru akalandira cholowa zimakhala bwino, ndipo nzeru zimapindulitsa anthu amene ali padziko lapansi. 12  Pakuti nzeru zimateteza+ monga mmene ndalama zimatetezera,+ koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.+ 13  Taona ntchito+ ya Mulungu woona, pakuti ndani angathe kuwongola zinthu zimene iye anazikhotetsa?+ 14  Pa tsiku labwino ukhale munthu wabwino,+ ndipo pa tsiku latsoka uzindikire kuti Mulungu woona anapanga masiku onsewa mofanana, ndi cholinga chakuti anthu asadziwe chilichonse chimene chidzachitike pambuyo pawo.+ 15  Ndaona zinthu zonse m’masiku anga opanda pake.+ Pali munthu wolungama amene amawonongeka akuchita zolungama, ndipo pali munthu woipa amene amakhala ndi moyo wautali akuchitabe zoipa.+ 16  Usakhale wolungama mopitirira muyezo+ kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri,+ kuopera kuti ungadzibweretsere chiwonongeko. 17  Usakhale woipa mopitirira muyezo, komanso usakhale wopusa.+ Uferenji mwamsanga? 18  Ndi bwino kuti usunge malangizo oyambawo, ndipo usasiye malangizo achiwiriwo.+ Pakuti munthu amene amaopa Mulungu adzamvera malangizo onsewa.+ 19  Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wamphamvu kuposa atsogoleri 10 amphamvu amene ali mumzinda. 20  Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa. 21  Komanso usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula, kuti ungamve wantchito wako akukunenera zoipa. 22  Pakuti mtima wako ukudziwa bwino kuti ngakhale iweyo wanenerapo anthu ena zoipa kambirimbiri.+ 23  Zonsezi ndinazifufuza mwanzeru ndipo ndinati: “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinatalikirana nane. 24  Zimene zinachitika kale n’zapatali ndiponso n’zozama kwambiri. Ndani angazimvetse?+ 25  Ineyo ndinaganiziranso mumtima mwanga+ kuti ndidziwe, ndifufuze, ndiponso ndifunefune nzeru.+ Ndinafunanso kudziwa zimene zimayambitsa zinthu,+ ndiponso kudziwa kuipa kwa kupusa ndi uchitsiru wa misala. 26  Ndipo izi n’zimene ndinapeza: Mkazi amene ali ngati ukonde wosakira nyama, amene mtima wake uli ngati khoka, amene manja ake ali ngati unyolo, ndi wowawa kuposa imfa. Munthu amakhala wabwino pamaso pa Mulungu woona akapulumuka kwa mkaziyo, koma amachimwa akagwidwa naye.+ 27  Wosonkhanitsa+ anati: “Taona zimene ndapeza. Ndafufuza chinthu chimodzichimodzi kuti ndidziwe tanthauzo la zonsezi,+ 28  limene ndakhala ndikulifunafuna koma osalipeza. Pa anthu 1,000, ndapezapo mwamuna mmodzi yekha wowongoka mtima, koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wowongoka mtima.+ 29  Zimene ndapeza n’zakuti, Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima, koma anthuwo asankha njira zina zambirimbiri.”

Mawu a M'munsi