Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 5:1-20

5  Samala mayendedwe+ ako ukapita kunyumba ya Mulungu woona. Ukapita kumeneko uzikamvetsera,+ osati uzikapereka nsembe monga mmene amachitira anthu opusa,+ pakuti iwo sadziwa kuti akuchita zoipa.+  Usamapupulume kulankhula, ndipo mtima wako+ usamafulumire kulankhula pamaso pa Mulungu woona,+ chifukwa Mulungu woona ali kumwamba+ koma iwe uli padziko lapansi. N’chifukwa chake suyenera kulankhula zambiri.+  Pakuti maloto amabwera chifukwa chochuluka zochita,+ ndipo kuchuluka kwa mawu kumachititsa munthu kulankhula zinthu zopusa.+  Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+  Kuli bwino kuti usalonjeze+ kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.+  Usalole kuti pakamwa pako pakuchimwitse,+ komanso usamanene kwa mngelo+ kuti unalakwitsa.+ Kodi Mulungu woona akwiyirenji chifukwa cha mawu ako n’kuwononga ntchito ya manja ako?+  Chifukwa chochuluka zochita pamakhala maloto,+ zinthu zachabechabe, ndi mawu ochuluka. Koma uziopa Mulungu woona yekha.+  Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zachiwawa ndi zopanda chilungamo+ zikuchitika m’chigawo cha dziko, usadabwe nazo.+ Pakuti wamkulu kuposa amene akuchita zimenezoyo+ akuona,+ ndipo pamwamba pa akuluakuluwo palinso ena akuluakulu kuposa iwowo.  Komanso, phindu la dziko lapansi ndi la munthu aliyense,+ chifukwa ngakhale mfumu imadalira kuti munda wake ulimidwe, kuti ipindule ndi zokolola za kumundako.+ 10  Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.+ Zimenezinso n’zachabechabe.+ 11  Zinthu zabwino zikachuluka ozidya amachulukanso,+ ndipo kodi mwiniwake wa zinthuzo amapindula chiyani kuposa kumangoziyang’ana ndi maso ake?+ 12  Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma+ ngakhale adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona. 13  Pali chinthu chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndaona padziko lapansi pano: Munthu kumangosunga chuma chake n’kudzapwetekedwa nacho.+ 14  Chumacho chimatha+ chifukwa cha zoipa zinazake zimene zachitika, kenako iye amabereka mwana wamwamuna pamene alibe chilichonse choti angapatse mwanayo ngati cholowa.+ 15  Monga mmene munthu anabadwira kuchokera m’mimba mwa mayi ake, adzapitanso wamaliseche+ ngati mmene anabwerera, ndipo palibe chilichonse chimene adzatenge+ pa ntchito yake imene anaigwira mwakhama. 16  Palinso chinthu china chomvetsa chisoni kwambiri: Monga mmene munthu anabwerera, adzapitanso chimodzimodzi. Kodi pali phindu lanji kwa munthu amene amachita khama kugwirira ntchito mphepo?+ 17  Komanso, masiku onse a moyo wake amadya chakudya chake mu mdima ndi kusautsika mtima kwakukulu,+ amadwala, ndiponso amakhala ndi nkhawa. 18  Chinthu chabwino kwambiri ndiponso chokongola chimene ine ndaona, n’chakuti munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala, chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta+ imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku onse a moyo wake amene Mulungu woona wam’patsa. Pakuti imeneyo ndiyo mphoto yake. 19  Komanso, munthu aliyense amene Mulungu woona wam’patsa chuma ndiponso zinthu zambiri,+ ndiye kuti wamulola kuti adye kuchokera pa zinthuzo.+ Wamulolanso kuti alandire mphoto yake ndi kusangalala chifukwa cha ntchito yake imene amaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 20  Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.+

Mawu a M'munsi