Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 3:1-22

3  Chilichonse chili ndi nthawi yake,+ ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake:  Pali nthawi yobadwa+ ndi nthawi ya kufa.+ Nthawi yobzala ndi nthawi yozula chimene chinabzalidwa.+  Nthawi yakupha+ ndi nthawi yochiritsa.+ Nthawi yogumula ndi nthawi yomanga.+  Nthawi yolira+ ndi nthawi yoseka.+ Nthawi yolira mofuula+ ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.+  Nthawi yotaya miyala+ ndi nthawi younjika miyala pamodzi.+ Nthawi yokumbatirana+ ndi nthawi yosakumbatirana.+  Nthawi yofunafuna+ ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika. Nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.+  Nthawi yong’amba+ ndi nthawi yosoka.+ Nthawi yokhala chete+ ndi nthawi yolankhula.+  Nthawi ya chikondi ndi nthawi ya chidani ndi munthu.+ Nthawi yankhondo+ ndi nthawi yamtendere.+  Kodi munthu wogwira ntchito mwakhama adzapeza phindu lanji pa ntchito yakeyo?+ 10  Ndaona ntchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+ 11  Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale+ kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.+ 12  Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+ 13  komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 14  Ndazindikira kuti zonse zimene Mulungu woona amapanga zimakhala mpaka kalekale.+ Palibe choti n’kuwonjezerapo kapena choti n’kuchotsapo.+ Mulungu woona ndi amene wapanga zimenezi,+ kuti anthu azimuopa.+ 15  Zimene zilipo zinalipo kale, ndipo zimene zidzachitike zinachitikapo kale.+ Mulungu woona+ amafunafuna kuchitira zabwino anthu amene akuzunzidwa.+ 16  Ine ndaonanso padziko lapansi pano kuti pamene panayenera kukhala chilungamo panali zoipa, ndipo pamene panayenera kuchitika zachilungamo panachitika zoipa.+ 17  Ine ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mulungu woona adzaweruza munthu wolungama ndi munthu woipa,+ pakuti iye ali ndi nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.”+ 18  Ineyo ndinanena mumtima mwanga kuti Mulungu woona adzasankhula ana a anthu. Zimenezi zidzawasonyeza kuti iwo ndi ofanana ndi zinyama.+ 19  Pakuti ana a anthu ali ndi mapeto, ndipo zinyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa.+ Mzimu wa zonsezi ndi umodzi,+ moti munthu saposa nyama, pakuti zonse n’zachabechabe. 20  Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+ 21  Ndani akudziwa ngati mzimu* wa ana a anthu umakwera m’mwamba, ndiponso ngati mzimu wa zinyama umatsika pansi?+ 22  Ine ndaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake,+ pakuti imeneyo ndi mphoto yake, popeza palibe amene adzam’bweretse kuti adzaone zimene zizidzachitika iye atafa.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 4.