Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 2:1-26

2  Ine ndinadziuza mumtima mwanga+ kuti: “Ndiyesereko kusangalala.+ Komanso ndisangalale ndi zinthu zabwino.”+ Ndipo ndinaona kuti zimenezonso zinali zachabechabe.  Ndinauza kuseka kuti: “Ndiwe wamisala!”+ ndipo kusangalala+ ndinakuuza kuti: “Uli ndi phindu lanji?”  Ndinafufuza ndi mtima wanga wonse kuti ndidziwe uchitsiru posangalatsa thupi langa ndi vinyo,+ pamene ndinali kutsogolera mtima wanga ndi nzeru.+ Ndinachita zimenezi kuti ndione ubwino umene ana a anthu amapeza pa zimene amachita padziko lapansi pano masiku onse a moyo wawo.+  Ndinachita zinthu zikuluzikulu.+ Ndinadzimangira nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+  Ndinadzipangira minda yokongola ndi malo obzalamo maluwa ndi mitengo.+ Mmenemu ndinabzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana.  Ndinadzipangira madamu a madzi+ kuti ndizithirira mitengo imene inali kumera m’nkhalango yanga.+  Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi antchito obadwira m’nyumba mwanga.+ Komanso, ndinali ndi ziweto zochuluka zedi, ng’ombe ndi nkhosa. Ziwetozo zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+  Ndinapezanso siliva ndi golide wambiri,+ ndi chuma chimene chimakhala ndi mafumu ndiponso chimene chimapezeka m’zigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi.+ Ndinalinso ndi akazi ambiri,+ omwe amasangalatsa mtima+ wa amuna.  Ndinali ndi zinthu zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ Komanso ndinali kuchitabe zinthu mwanzeru.+ 10  Chilichonse chimene maso anga anali kupempha sindinali kuwamana.+ Mtima wanga sindinaumane chosangalatsa cha mtundu uliwonse. Ndinasangalalanso ndi ntchito yonse imene ndinaigwira mwakhama.+ Imeneyi ndiyo inali mphoto yanga ya ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+ 11  Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+ 12  Ineyo ndinaganizaganiza kuti nzeru n’chiyani,+ misala n’chiyani, ndipo uchitsiru n’chiyani.+ Kodi munthu wochokera kufumbi amene wabwera pambuyo pa mfumu angachite chiyani? Zimene angachite n’zimene anthu ena anachita kale. 13  Ndinaona kuti nzeru zili ndi phindu lalikulu kuposa uchitsiru+ monga mmene kuwala kulili ndi phindu lalikulu kuposa mdima.+ 14  Aliyense wanzeru maso ake amaona bwino,+ koma wopusa amangoyendabe mu mdima waukulu.+ Ineyo ndazindikira kuti onsewa mapeto awo ndi amodzi.+ 15  Ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mapeto ngati a munthu wopusa+ adzagweranso ineyo ndithu.”+ Choncho kodi ineyo ndinavutikiranji kukhala wanzeru kwambiri+ pa nthawi imene ija? Ndipo ndinanena mumtima mwanga kuti: “Izinso n’zachabechabe.” 16  Pakuti munthu wanzeru, mofanana ndi wopusa, sadzakumbukiridwa mpaka kalekale.+ M’masiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalidwa. Ndipo kodi wanzeru adzafa motani? Adzafa mofanana ndi wopusa.+ 17  Ine ndinadana ndi moyo+ chifukwa ndinaona kuti ntchito imene yachitidwa padziko lapansi pano ndi yosautsa mtima.+ Pakuti zonse zinali zachabechabe ndipo kuchita zimenezi kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18  Ineyo ndinadana ndi ntchito yonse yovuta imene ndinali kugwira padziko lapansi pano,+ imene ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19  Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikira ndiponso zimene ndinazichita mwanzeru padziko lapansi pano.+ Zimenezinso n’zachabechabe. 20  Ineyo ndinayamba kutaya mtima+ poganizira ntchito yanga yonse yovuta imene ndinaigwira mwakhama padziko lapansi pano. 21  Pakuti pali munthu amene ntchito yake yovuta waigwira mwanzeru, mozindikira ndiponso waigwira bwino.+ Koma zonse zimene anapeza zidzaperekedwa kwa munthu amene sanagwire mwakhama ntchito ngati imeneyo.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo n’zomvetsa chisoni kwambiri.+ 22  Pakuti munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene waigwira mwakhama, ndiponso imene wasautsika nayo mtima poigwira padziko lapansi pano?+ 23  Masiku ake onse, ntchito yakeyo imamubweretsera zowawa ndi zokhumudwitsa.+ Komanso usiku mtima wake sugona.+ Izinso n’zachabechabe. 24  Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Ineyo ndaona kuti zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.+ 25  Pakuti ndani amadya+ bwino ndi kumwa zabwino kuposa ine?+ 26  Munthu wabwino pamaso pa Mulungu,+ Mulunguyo amam’patsa nzeru, kudziwa zinthu, ndi kusangalala.+ Koma wochimwa amam’patsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene ali wabwino pamaso pa Mulungu woona.+ Zimenezinso n’zachabechabe ndipo kuli ngati kuthamangitsa mphepo.+

Mawu a M'munsi