Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 11:1-10

11  Tumiza mkate wako+ pamadzi,+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+  Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7, ngakhale 8,+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.+  Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi,+ ndipo mtengo+ ukagwera kum’mwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.  Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.+  Monga momwe sudziwira mmene mzimu umagwirira ntchito m’thupi la mwana amene ali m’mimba mwa mayi ake,+ momwemonso sudziwa ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+  Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino,+ kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.  Kuwala n’kokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa.+  Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, m’zaka zonsezo azisangalala.+ Iye akumbukire masiku a mdima,+ ngakhale atakhala ambiri. Tsiku lililonse limene likubwera n’lachabechabe.+  Mnyamatawe, sangalala+ ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako. Yenda m’njira za mtima wako ndiponso motsatira zimene maso ako akuona.+ Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza chifukwa cha zonsezi.+ 10  Choncho chotsa zosautsa mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku tsoka,+ chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo n’zachabechabe.+

Mawu a M'munsi