Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mlaliki 1:1-18

1  Mawu a wosonkhanitsa anthu, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu.  Wosonkhanitsa anthu wanena kuti: “Zachabechabe!+ Zinthu zonse n’zachabechabe!”+  Kodi munthu amapeza phindu lanji pa ntchito yake yonse yovuta, imene amaigwira+ mwakhama padziko lapansi pano?*+  M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwera,+ koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.*+  Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa,+ kenako limathamanga mwawefuwefu kupita kumalo ake kuti likatulukenso.  Mphepo imapita kum’mwera ndipo imazungulira n’kupita kumpoto.+ Iyo imangozungulirazungulira+ mpaka imabwereranso kumene inayambira kuzungulira.+  Mitsinje*+ yonse imapita kunyanja+ koma nyanjayo sidzaza.+ Mitsinjeyo imabwerera kumalo kumene inachokera kuti ikayambirenso kuyenda.+  Zinthu zonse n’zotopetsa,+ ndipo palibe angazifotokoze. Diso silikhuta n’kuona,+ ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.+  Zimene zinalipo n’zimene zidzakhaleponso+ ndipo zimene zinachitidwa n’zimene zidzachitidwenso. Choncho palibe chatsopano padziko lapansi pano. 10  Kodi chilipo chimene munthu anganene kuti: “Wachiona ichi, n’chatsopanotu chimenechi?” Ayi, chakhalapo kuyambira kalekale.+ Zimene zilipo panopa, zinalipo ife tisanakhaleko. 11  Anthu akale sakumbukiridwa, ndipo amene adzakhalepo m’tsogolo sadzakumbukiridwanso.+ Iwowanso sadzakumbukiridwa ndi amene adzakhalepo m’tsogolo mwawo.+ 12  Ine wosonkhanitsa, ndinali mfumu ya Isiraeli ku Yerusalemu. 13  Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndifunefune ndi kufufuza nzeru mogwirizana ndi zonse zimene zachitidwa padziko lapansi, kutanthauza ntchito yosautsa mtima imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+ 14  Choncho ndinaona ntchito zonse zimene zinachitidwa padziko lapansi pano,+ ndipo ndinapeza kuti zonse ndi zachabechabe ndiponso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 15  Chinthu chokhota sichingawongoledwe ndipo chimene palibe sichingawerengedwe n’komwe. 16  Ineyo ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Ine ndili ndi nzeru zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo. Komanso mtima wanga wapeza nzeru zambiri ndiponso wadziwa zinthu zambiri.” 17  Ndinapereka mtima wanga kuti udziwe nzeru ndiponso misala,+ ndipo ndadziwa uchitsiru.+ Pochita zimenezi ndazindikira kuti zimenezinso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18  Pakuti nzeru zikachuluka pamachulukanso kukhumudwa,+ choncho amene amadziwa zinthu zambiri amakhalanso ndi zopweteka zambiri.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “pansi pa dzuwa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mitsinje yoyenda nthawi yozizira.”