Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 6:1-35

6  Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza, ngati wagwirana chanza ndi mlendo pochita mgwirizano,+  ngati wakodwa ndi mawu a m’kamwa mwako,+ ngati wagwidwa ndi mawu a m’kamwa mwako,  uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse, pakuti wagwa m’manja mwa mnzako: Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+  Maso ako asapeze tulo, ndipo maso ako owala asagone.+  Dzipulumutse ngati insa m’manja mwa wosaka, ndiponso ngati mbalame m’manja mwa wosaka mbalame.+  Pita kwa nyerere+ waulesi iwe,+ ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.  Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,  imakonza chakudya chake m’chilimwe.+ Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola.  Kodi ugonabe mpaka liti, waulesiwe?+ Udzuka nthawi yanji kutulo tako?+ 10  Ukapitiriza kugona pang’ono, ukapitiriza katulo pang’ono, ukapitiriza kupinda manja pang’ono pogona,+ 11  umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,+ ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+ 12  Munthu wopanda pake, wochita zopweteka anzake, amayenda ndi mawu opotoka.+ 13  Amatsinzinira ena ndi diso lake,+ amapanga zizindikiro ndi phazi lake, ndiponso amapanga zizindikiro ndi zala zake.+ 14  Mumtima mwake muli zopotoka. Nthawi zonse amakhala akukonza zoipa.+ Amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15  N’chifukwa chake tsoka lake lidzabwere mwadzidzidzi.+ Adzathyoledwa modzidzimutsa, ndipo sadzachira. 16  Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.+ Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo: 17  Maso odzikweza, lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, 18  mtima wokonzera ena ziwembu, mapazi othamangira kukachita zoipa,+ 19  mboni yachinyengo yonena mabodza, ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale. 20  Mwana wanga, sunga lamulo la bambo ako,+ ndipo usasiye malangizo a mayi ako. 21  Ulimange pamtima pako nthawi zonse ndipo ulimange m’khosi mwako.+ 22  Lidzakutsogolera ukamayenda,+ lidzakulondera ukamagona,+ ndipo ukadzuka, lidzakusamalira. 23  Pakuti lamulolo ndilo nyale,+ ndipo malangizo ndiwo kuwala,+ komanso kudzudzula* kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo,+ 24  kuti kukuteteze kwa mkazi woipa,+ komanso ku lilime losalala la mkazi wachilendo.+ 25  Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+ Asakukope ndi maso ake owala,+ 26  pakuti munthu amafika potsala ndi mkate wozungulira umodzi wokha chifukwa cha hule,+ koma mkazi wamwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.+ 27  Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28  Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29  N’chimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake. Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa. 30  Anthu sanyoza munthu wakuba, akaba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31  Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7. Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake. 32  Aliyense wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru mumtima mwake.+ Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.+ 33  Adzapeza tsoka ndi manyazi,+ ndipo kunyozeka kwake sikudzafufutika. 34  Pakuti nsanje ya mwamuna imautsa mkwiyo wake, ndipo sadzamva chisoni pa tsiku lobwezera. 35  Iye sadzavomera dipo* lamtundu uliwonse, ndipo sadzalola ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.