Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 5:1-23

5  Mwana wanga, mvetsera nzeru zanga.+ Tchera makutu ako ku zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kuzindikira,+  kuti uteteze kuganiza bwino,+ ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+  Pakuti milomo ya mkazi wachilendo imakha uchi ngati chisa cha njuchi+ ndipo m’kamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+  Koma zotsatirapo zochokera kwa iye n’zowawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+ N’zakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+  Mapazi ake amatsikira ku imfa.+ Miyendo yake imalowera ku Manda.+  Iye saganizira njira ya moyo.+ Amangoyendayenda panjira zake osadziwa kumene akupita.+  Tsopano ananu ndimvereni,+ ndipo musapatuke pa mawu otuluka m’kamwa mwanga.+  Njira yako ikhale kutali ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+  kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+ kapena kupereka zaka zako ku zinthu zankhanza.+ 10  Ndiponso kuti alendo asakhute mphamvu zako,+ kuti zinthu zimene unazipeza movutikira* zisakhale m’nyumba ya mlendo,+ 11  komanso kuti usadzabuule m’tsogolo+ mnofu ndi thupi lako zikadzafika ku mapeto kwake.+ 12  Pa nthawiyo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine,+ ndipo mtima wanga sunkavomereza kudzudzula.+ 13  Sindinamvere mawu a alangizi anga,+ ndipo sindinatchere khutu kwa aphunzitsi anga.+ 14  N’chifukwa chake mosayembekezeka ndinagwera m’zinthu zoipa zamtundu uliwonse,+ ndipo ndinachita manyazi pamaso pa mpingo wonse.”+ 15  Imwa madzi ochokera m’chitsime chako, komanso madzi oyenderera kuchokera pakati pa chitsime chako.+ 16  Kodi akasupe ako amwazike panja,+ ndipo mitsinje yako yamadzi imwazike m’mabwalo a mumzinda? 17  Zimenezi zikhale zako zokha osatinso za alendo amene ali nawe.+ 18  Kasupe wa madzi ako akhale wodalitsidwa,+ ndipo usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.+ 19  Iye akhale ngati mbawala yaikazi yokondedwa ndiponso ngati mbuzi yokongola ya m’mapiri.+ Mabere ake akukhutiritse nthawi zonse.+ Nthawi zonse uzikhala wokondwa kwambiri ndi chikondi chake.+ 20  Chotero pali chifukwa chanji choti usangalalire ndi mkazi wachilendo mwana wanga, kapena choti ukumbatirire chifuwa cha mkazi wina?+ 21  Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,+ ndipo iye amaonetsetsa njira zake zonse.+ 22  Woipa adzagwidwa ndi zolakwa zake zomwe,+ ndipo adzamangidwa m’zingwe za tchimo lake lomwe.+ 23  Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,+ ndiponso chifukwa chakuti amasocheretsedwa ndi zopusa zake zochuluka.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “zimene unazipeza ukumva kupweteka.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.