Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 30:1-33

30  Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake, mwamuna wamphamvu. Mawuwa anali uthenga wamphamvu+ womwe iye analankhula ndi Itiyeli, ndi Itiyeli ndiponso Ukali, kuti:  Ine ndine wopanda nzeru kuposa munthu wina aliyense,+ ndipo sindimvetsa zinthu monga mmene anthu onse amamvetsetsera.+  Inetu ndilibe nzeru,+ ndipo sindidziwa nzeru zimene zili ndi Woyera Koposa.+  Ndani amene anakwerapo kumwamba n’kubwerako?+ Ndani anasonkhanitsapo mphepo m’manja mwake?+ Ndani anamangapo madzi munsalu?+ Ndani anaika malekezero onse a dziko lapansi?+ Dzina lake ndani?+ Nanga mwana wake dzina lake ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.+  Mawu alionse a Mulungu ndi oyera.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+  Usawonjezere kanthu pa mawu ake+ kuti angakudzudzule ndiponso kuti ungakhale wabodza.+  Ndikukupemphani zinthu ziwiri.+ Musandikanize ndisanafe.+  Zachinyengo ndi mawu onama muwaike kutali ndi ine.+ Musandipatse umphawi kapena chuma.+ Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya,+  kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani+ kuti: “Kodi Yehova ndani?”+ ndiponso kuti ndisasauke n’kukaba ndi kunyozetsa dzina la Mulungu wanga.+ 10  Usanenere wantchito zoipa kwa mbuye wake,+ kuti angakutemberere ndiponso kuti ungakhale ndi mlandu.+ 11  Pali m’badwo umene umatemberera ngakhale abambo awo ndiponso umene sudalitsa ngakhale amayi awo.+ 12  Pali m’badwo umene umadziona kuti ndi woyera,+ koma sunasambe kuti uchotse ndowe zake.+ 13  Pali m’badwo umene maso ake ali pamwamba kwambiri, ndiponso umene maso ake owala ali odzikweza.+ 14  Pali m’badwo umene mano ake ali ngati malupanga ndiponso umene nsagwada zake zili ngati mipeni yophera nyama,+ kuti m’badwowo udye osautsidwa onse a padziko lapansi ndiponso anthu osauka pakati pa anthu.+ 15  Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti: “Tipatseni! Tipatseni!” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta ndiponso zinthu zinayi zimene sizinena kuti: “Ndakhuta!” Zinthuzo ndi izi: 16  Manda,+ mimba yosabereka,+ nthaka imene sikhuta madzi,+ ndiponso moto+ umene sunena kuti: “Ndakhuta!”+ 17  Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya. 18  Pali zinthu zitatu zimene n’zodabwitsa kwambiri kwa ine, ndiponso zinthu zinayi zimene sindizimvetsa. Zinthuzo ndi izi: 19  Njira ya chiwombankhanga m’mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakatikati pa nyanja,+ ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.+ 20  Nayi njira ya mkazi wachigololo: Iye amadya n’kupukuta pakamwa pake ndipo amanena kuti: “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+ 21  Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansi ndiponso zinthu zinayi zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthuzo ndi izi: 22  Kapolo akamalamulira monga mfumu,+ munthu wopusa akakhuta,+ 23  mkazi wodedwa akakwatiwa,+ ndiponso mtsikana wantchito akatenga malo a mbuye wake wamkazi.+ 24  Pali zinthu zinayi zomwe ndi zing’onozing’ono kwambiri padziko lapansi koma n’zanzeru mwachibadwa:+ 25  Nyerere si zamphamvu,+ koma zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe.+ 26  Mbira+ si nyama zamphamvu koma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+ 27  Dzombe+ lilibe mfumu koma limauluka lonse litagawikana m’magulumagulu.+ 28  Nalimata*+ amagwira zinthu ndi manja ake ndipo amapezeka m’nyumba yaikulu yachifumu. 29  Pali zinthu zitatu zimene zimayenda molemekezeka ndiponso zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira. Zinthuzo ndi izi: 30  Mkango, umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire ndiponso umene suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo,+ 31  galu wosaka kapena mbuzi yamphongo, ndiponso mfumu imene ikutsogolera asilikali ake.+ 32  Ngati wachita zinthu zopusa n’kudzikweza,+ ndiponso ngati watsimikiza mtima wako kuti uchite zimenezo, gwira pakamwa pako.+ 33  Pakuti mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta, mphuno ukaifinya imatulutsa magazi, ndipo kutulutsa mkwiyo kumayambitsa mkangano.+

Mawu a M'munsi

“Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala m’madzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama n’kumayamwa magazi.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
“Nalimata” ndi kabuluzi kakang’ono komwe kamakonda kukhala m’nyumba, koonekera matumbo.