Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 29:1-27

29  Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+  Olungama akachuluka, anthu amasangalala,+ koma aliyense woipa akayamba kulamulira, anthu amabuula.+  Munthu wokonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+ koma woyenda ndi mahule amawononga zinthu zamtengo wapatali.+  Pochita zinthu zachilungamo, mfumu imachititsa dziko kulimba,+ koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.+  Mwamuna wamphamvu amene amanena zabwino za mnzake mokokomeza,+ akuyalira ukonde mapazi ake.+  Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+ koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+  Wolungama amaganizira za mlandu wa anthu onyozeka.+ Woipa saganizira zimenezo.+  Anthu olankhula modzitama amabutsa mkwiyo wa mzinda,+ koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+  Munthu wanzeru akakhala pa mlandu ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso n’kumaseka, ndipo munthu wanzeruyo sapeza mpumulo.+ 10  Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi aliyense wopanda cholakwa,+ koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.+ 11  Wopusa amatulutsa mkwiyo* wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.+ 12  Mtsogoleri akamamvera mabodza, onse omutumikira adzakhala oipa.+ 13  Munthu wosauka ndiponso munthu wozunza ena n’chimodzimodzi,+ koma Yehova amawalitsa maso a onsewa.+ 14  Mfumu ikamaweruza anthu onyozeka mwachilungamo,+ mpando wake wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.+ 15  Chikwapu ndi chidzudzulo n’zimene zimapereka nzeru,+ koma mwana womulekerera adzachititsa manyazi mayi ake.+ 16  Oipa akachuluka, machimo amachuluka, koma olungama adzawaona oipawo akugwa.+ 17  Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumulo ndiponso adzasangalatsa kwambiri moyo wako.+ 18  Popanda kutsogozedwa ndi Mulungu, anthu amatayirira,+ koma odala ndi amene amasunga malamulo.+ 19  Wantchito salola kusintha ndi mawu okha,+ chifukwa amamvetsa koma satsatira.+ 20  Kodi waona munthu wopupuluma m’mawu ake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.+ 21  Ngati munthu akusasatitsa* wantchito wake kuyambira ali mwana, akadzakula adzakhala wosayamika. 22  Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano,+ ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+ 23  Kudzikuza kwa munthu wochokera kufumbi kudzamutsitsa,+ koma wa mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+ 24  Wochita ubwenzi ndi mbala akudana ndi moyo wake.+ Iye angamve lumbiro lokhudza temberero, koma osakanena chilichonse.+ 25  Kuopa anthu n’kumene kumatchera msampha,+ koma wokhulupirira Yehova adzatetezedwa.+ 26  Anthu ambiri amafuna kuonana ndi mtsogoleri,+ koma chiweruzo cha munthu chimachokera kwa Yehova.+ 27  Munthu wopanda chilungamo amakhala wonyansa kwa anthu olungama,+ ndipo munthu wowongoka m’njira yake amakhala wonyansa kwa munthu woipa.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mzimu.”
Munthu wosasatitsidwa ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.