Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 28:1-28

28  Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,+ koma olungama ali ngati mkango wamphamvu umene umakhala wolimba mtima.+  Anthu okhala m’dziko akamachimwa pamakhala akalonga ambiri otsatizanatsatizana,+ koma chifukwa cha munthu wozindikira, wodziwa zinthu zoyenera kuchita, kalonga amakhala kwa nthawi yaitali.+  Mwamuna wamphamvu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+ ali ngati mvula imene imakokolola zinthu moti sipakhalanso chakudya.  Anthu osiya chilamulo akamatamanda munthu woipa,+ anthu amene amasunga chilamulo amawaukira.+  Anthu okonda kuchita zoipa sangamvetse chilungamo, koma amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.+  Munthu wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika, ali bwino kuposa munthu aliyense woyenda m’njira zokhota, ngakhale ali wolemera.+  Mwana womvetsa zinthu amasunga malamulo,+ koma wochita ubwenzi ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+  Munthu amene amachulukitsa zinthu zamtengo wapatali kuchokera ku chiwongoladzanja ndi katapira,*+ amangosungira zinthuzo munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+  Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo,+ ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+ 10  Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima+ kuti ayende m’njira yoipa, adzagwera m’dzenje lake lomwe.+ Koma anthu osalakwa adzapeza zabwino.+ 11  Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru m’maso mwake,+ koma munthu wonyozeka amene ali wozindikira zinthu amam’fufuza n’kudziwa zoona zake.+ 12  Anthu olungama akamasangalala+ zimakhala bwino kwambiri, koma anthu oipa akamalamulira, munthu amadzisintha maonekedwe.+ 13  Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+ 14  Wodala ndi munthu amene amaopa Mulungu nthawi zonse,+ koma woumitsa mtima wake adzagwera m’tsoka.+ 15  Mtsogoleri woipa wolamulira anthu onyozeka ali ngati mkango wobangula ndiponso chimbalangondo chimene chikubwera kudzakuluma.+ 16  Mtsogoleri amene ali wosazindikira kwenikweni amakhalanso wakatangale kwambiri,+ koma munthu wodana ndi phindu lachinyengo+ adzachulukitsa masiku ake. 17  Munthu wolemedwa ndi mlandu wokhetsa magazi a munthu adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.+ Anthu asamugwire n’cholinga choti amuletse. 18  Woyenda mosalakwa adzapulumutsidwa,+ koma woyenda m’njira zokhota adzagwa mwadzidzidzi.+ 19  Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+ ndipo amene amafunafuna zinthu zopanda phindu adzakhala ndi umphawi waukulu.+ 20  Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+ 21  Si bwino kukondera.+ Si bwinonso kuti mwamuna wamphamvu achimwe chifukwa cha kachidutswa ka mkate. 22  Munthu wanjiru amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali,+ koma sadziwa kuti umphawi udzamugwera. 23  Wodzudzula munthu,+ patsogolo pake adzakondedwa kwambiri kuposa amene amakokomeza ndi lilime lake ponena zinthu zabwino za wina. 24  Wobera bambo ake ndi mayi ake+ n’kumanena kuti: “Si kulakwa,”+ amakhala mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko. 25  Munthu wonyada amayambitsa mikangano,+ koma wodalira Yehova adzanenepa.+ 26  Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa,+ koma woyenda mwanzeru ndi amene adzapulumuke.+ 27  Wopatsa zinthu munthu wosauka sadzasowa kanthu,+ koma wophimba maso ake adzapeza matemberero ambiri.+ 28  Oipa akamalamulira, munthu amadzibisa.+ Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.