Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 25:1-28

25  Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya mfumu ya Yuda+ anakopa, ndi iyi:  Ulemerero wa Mulungu ndiwo kusunga chinsinsi,+ ndipo ulemerero wa mafumu ndiwo kufufuza bwino nkhani.+  Kutalika kwa kumwamba,+ kuzama kwa dziko lapansi,+ ndiponso mtima wa mafumu, zonsezi n’zosatheka kuzifufuza.+  Siliva akachotsedwa zotsalira pomuyenga, yense adzatuluka woyengeka bwino.+  Woipa akachotsedwa pamaso pa mfumu,+ mpando wake wachifumu udzakhazikitsidwa ndi chilungamo.+  Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+ ndipo usaime pamalo a anthu olemekezeka,+  pakuti ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti: “Bwera pamwamba pano,”+ kusiyana n’kuti ikutsitse pamaso pa munthu wolemekezeka amene wamuona ndi maso ako.+  Usamapite kukazenga mlandu mofulumira, pakuti udzachita chiyani pamapeto pake mnzakoyo akakuchititsa manyazi?+  Kambirana mlandu wako ndi mnzako,+ ndipo usaulule chinsinsi cha munthu wina,+ 10  kuti amene akumvetsera angakuchititse manyazi ndiponso kuti nkhani yoipa imene iwe wanena ingavute kuiiwala. 11  Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.+ 12  Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo* yagolide, ndiponso ngati chokongoletsera chagolide wapadera.+ 13  Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aituma ili ngati kuzizira kwa chipale chofewa+ pa tsiku lokolola, chifukwa imatsitsimula moyo wa ambuye ake.+ 14  Munthu wodzitama kuti wapereka mphatso koma sanapereke, ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.+ 15  Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.+ 16  Ukapeza uchi udye wokukwanira,+ kuti usadye wambiri n’kuusanza.+ 17  Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako, kuti angatope nawe n’kuyamba kudana nawe. 18  Munthu wonenera mnzake umboni wonama ali ngati chibonga cha kunkhondo, lupanga, ndi muvi wakuthwa.+ 19  Kudalira munthu amene amachita zachinyengo pa tsiku la masautso kuli ngati dzino lothyoka ndi phazi lotsimphina.+ 20  Wovula malaya pa tsiku lozizira ali ngati vinyo wowawasa wothiridwa mu soda, ndiponso ngati woimbira nyimbo munthu wa mtima wachisoni.+ 21  Ngati munthu wodana nawe ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse madzi akumwa,+ 22  pakuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,+ ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.+ 23  Mphepo yochokera kumpoto imabweretsa mvula yambiri. Imakhala ngati kuti yabereka mvulayo ndi ululu wa pobereka.+ Chotero munthu wa lilime loulula chinsinsi amakhala ndi nkhope yonyozedwa.+ 24  Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba, kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+ 25  Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+ ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.+ 26  Munthu wolungama akamanjenjemera pamaso pa munthu woipa, amakhala ngati kasupe woipitsidwa ndiponso chitsime chowonongedwa.+ 27  Kudya uchi wambiri si bwino,+ ndipo anthu akamafunafuna okha ulemerero, kodi umenewo ndi ulemererodi?+ 28  Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masikiyo.”