Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 24:1-34

24  Usamasirire anthu oipa,+ ndipo usamasonyeze kuti ukusirira kukhala pagulu lawo,+  chifukwa mtima wawo umangokhalira kuganizira zolanda zinthu za ena, ndipo milomo yawo imangokhalira kunena zobweretsera ena mavuto.  Nzeru zimamanga banja la munthu,+ ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.+  Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda zamkati mwa nyumba zidzaze ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.  Munthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwanzeru ndiye mwamuna wamphamvu,+ ndipo munthu wodziwa zinthu amachulukitsa mphamvu zake.+  Iweyo udzatha kumenya nkhondo yako potsatira malangizo anzeru,+ ndipo pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+  Kwa munthu wopusa, nzeru zenizeni n’chinthu chapatali.+ Iye satsegula pakamwa pake pachipata cha mzinda.  Aliyense wokonzera anzake ziwembu adzatchedwa katswiri wa maganizo oipa.+  Khalidwe lotayirira lobwera chifukwa cha kupusa limakhala tchimo,+ ndipo munthu wonyoza, anthu amanyansidwa naye.+ 10  Ukafooka pa tsiku la masautso,+ mphamvu zako zidzakhala zochepa. 11  Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe, ndipo amene akudzandira popita ku imfa, chonde uwabweze.+ 12  Ukanena kuti: “Ifetu izi sitinali kuzidziwa,”+ kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimenezo? Ndipo kodi amene amayang’anitsitsa moyo wako sadziwa zimenezo+ n’kubwezera munthu wochokera kufumbi mogwirizana ndi ntchito yake?+ 13  Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino, ndipo uchi wotsekemera wochokera pazisa za njuchi uuike m’kamwa mwako.+ 14  M’njira yomweyo, dziwa nzeru kuti upindule.+ Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+ 15  Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pamalo ake okhala. Usamasakaze malo ake okhala,+ 16  pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.+ Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa. 17  Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere, 18  kuti Yehova angaone ndipo zingamuipire m’maso mwake n’kuchotsa mkwiyo wake pamdani wakoyo.+ 19  Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa. Usamasirire anthu oipa,+ 20  pakuti aliyense woipa alibe tsogolo,+ ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+ 21  Mwana wanga uziopa Yehova ndiponso mfumu. Usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe, 22  pakuti tsoka lawo lidzagwa mwadzidzidzi, ndipo ndani angadziwe za kufafanizika kwa anthu ofuna kuti zinthu zisinthe?+ 23  Mawu awanso akupita kwa anthu anzeru: Si bwino kukondera poweruza. 24  Munthu amene amauza woipa kuti: “Ndiwe wolungama,” anthu adzamutemberera, ndipo mitundu ya anthu idzamutsutsa. 25  Koma anthu omudzudzula zinthu zidzawayendera bwino, ndipo adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+ 26  Woyankha mosapita m’mbali adzapsompsona milomo ya anthu.+ 27  Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo konza munda wako. Ukatero ukamange banja lako. 28  Usakhale mboni yotsutsana ndi mnzako popanda umboni, chifukwa ukhoza kukhala wopusa ndi milomo yako.+ 29  Usanene kuti: “Ndim’chitira zimene iye anandichitira.+ Aliyense ndizim’bwezera mogwirizana ndi zimene anachita.”+ 30  Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi+ ndiponso pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+ 31  Ndipo ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.+ Zitsamba zoyabwa zinali paliponse m’mundamo komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+ 32  Choncho ine nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,+ ndipo ndinaphunzirapo* kuti:+ 33  Ukati, “Ndigoneko pang’ono, ndibeko katulo pang’ono, ndipindeko manja pang’ono pogona,”+ 34  umphawi wako ndithu udzabwera ngati wachifwamba ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.