Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 23:1-35

23  Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uzionetsetsa zimene zili pamaso pako,+  ndipo uzidziletsa* ngati uli wadyera.+  Usasonyeze kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma, chifukwa ndi zakudya zachinyengo.+  Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.+ Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.+  Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka?+ Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.+  Usamadye chakudya cha aliyense womana,+ kapena kusonyeza kuti ukulakalaka zakudya zake zokoma.+  Pakuti iye ali ngati munthu amene wawerengetsera bwino zinthu mumtima mwake. Amakuuza kuti:+ “Idya, imwa,” koma salankhula ndi mtima wonse.+  Nthongo imene wadya udzaisanza, ndipo mawu ako abwino adzakhala atapita pachabe.+  Usalankhule m’makutu mwa munthu wopusa,+ chifukwa iye adzanyoza mawu ako anzeru.+ 10  Usasunthire kumbuyo malire akalekale,+ ndipo usalowe m’munda mwa ana amasiye.*+ 11  Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+ 12  Bweretsa mtima wako kuti umve malangizo, ndi khutu lako kuti limve mawu a munthu wodziwa zinthu.+ 13  Usam’mane chilango* mwana.+ Ngakhale utam’kwapula ndi chikwapu, sangafe ayi. 14  Um’kwapule ndi chikwapu, kuti upulumutse moyo wake ku Manda.+ 15  Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,+ ndithu mtima wanga udzasangalala.+ 16  Impso zanga zidzasangalala milomo yako ikamalankhula zowongoka.+ 17  Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+ koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+ 18  Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+ ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+ 19  Iwe mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru, ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino.+ 20  Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri,+ ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka.+ 21  Chifukwa chidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka,+ ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.+ 22  Mvera bambo ako amene anakubereka,+ ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ 23  Gula choonadi+ ndipo usachigulitse. Gula nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.+ 24  Bambo wa munthu wolungama ndithu adzasangalala.+ Bambo wobereka mwana wanzeru adzakondwera naye.+ 25  Bambo ako ndi mayi ako adzakondwera, ndipo mayi amene anakubereka adzasangalala.+ 26  Mwana wanga, ndipatse mtima wako, ndipo maso ako asangalale ndi njira zanga.+ 27  Pakuti hule lili ngati dzenje lakuya,+ ndipo mkazi wachilendo ali ngati chitsime chopapatiza. 28  Ndithudi iye mofanana ndi wachifwamba,+ amabisalira anthu panjira, ndipo amachulukitsa amuna achinyengo.+ 29  Ndani ali ndi tsoka? Ndani sakhazikika maganizo? Ndani ali pa mikangano?+ Ndani ali ndi nkhawa? Ndani ali ndi zilonda popanda chifukwa? Ndani ali ndi maso ofiira? 30  Ndi anthu amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo,+ amene amabwera kudzafunafuna vinyo wosakaniza.+ 31  Usayang’ane vinyo akamaoneka wofiira, akamanyezimira m’kapu, akamatsetserekera kukhosi mwamyaa! 32  Kumapeto kwake amaluma ngati njoka,+ ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri.+ 33  Maso ako adzaona zinthu zachilendo, ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota.+ 34  Ndithu udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja, komanso ngati munthu amene wagona pamwamba pa mlongoti wa ngalawa.+ 35  Udzati: “Andimenya koma sindinavulale, andikuntha koma sindinadziwe. Kodi ndidzuka nthawi yanji+ kuti ndikamwenso wina?”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “uziika mpeni pakhosi pako.”
Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.