Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 21:1-31

21  Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova.+ Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.+  Njira iliyonse ya munthu imaoneka yowongoka m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza mitima.+  Kuchita zinthu zoyenera ndi zachilungamo kumamusangalatsa kwambiri Yehova, kuposa kupereka nsembe.+  Maso odzikweza ndi mtima wodzikuza+ ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi tchimo.+  Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira,+ koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.+  Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira.+ Anthu ochita zinthu mwa njira imeneyi akufunafuna imfa.+  Kulanda zinthu za ena kumene anthu oipa amachita n’kumene kudzawawononge,+ chifukwa akana kuchita chilungamo.+  Njira ya mlendo imakhala yokhota,+ koma munthu woyera amachita zowongoka.+  Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba,+ kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+ 10  Moyo wa munthu woipa umalakalaka zoipa,+ ndipo iye akaona mnzake samumvera chisoni.+ 11  Mwa kulipiritsa munthu wonyoza, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru.+ Munthu wanzeru akapatsidwa malangizo, amadziwa zinthu.+ 12  Mulungu wolungama amayang’ana nyumba ya munthu woipa,+ ndipo anthu oipa amawagwetsa kuti akumane ndi tsoka.+ 13  Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,+ nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+ 14  Mphatso yoperekedwa mobisa imathetsa mkwiyo,+ ndipo chiphuphu chopereka mobisa chimathetsa+ ukali waukulu. 15  Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzakumana ndi zoipa.+ 16  Munthu wochoka pa njira yochita zinthu mozindikira,+ adzapumula mumpingo wa anthu akufa.+ 17  Wokonda zosangalatsa adzakhala munthu wosauka.+ Wokonda vinyo ndi mafuta sadzapeza chuma.+ 18  Munthu woipa ndiye dipo la wolungama,+ ndipo munthu wochita zachinyengo amalowa m’malo mwa anthu owongoka mtima.+ 19  Kuli bwino kukhala m’chipululu kusiyana ndi kukhala mokhumudwa ndi mkazi wolongolola.+ 20  Chuma chosiririka ndiponso mafuta zimakhala pamalo a munthu wanzeru,+ koma wopusa amazimeza.+ 21  Amene akufunafuna chilungamo+ ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+ 22  Wanzeru amakwera mzinda wa anthu amphamvu, kuti athetse mphamvu imene mzindawo umadalira.+ 23  Wosunga pakamwa pake ndiponso lilime lake akuteteza moyo wake ku masautso.+ 24  Munthu amene amadzikuza akapsa mtima, amatchedwa wodzikuza, wonyada ndi wodzitama.+ 25  Zolakalaka za munthu waulesi zidzamupha, chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+ 26  Tsiku lonse amaoneka kuti akulakalaka kwambiri chinachake, koma wolungama amapatsa ndipo saumira chilichonse.+ 27  Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+ 28  Mboni yonama idzawonongedwa,+ koma munthu amene amamvetsera adzalankhula kwamuyaya.+ 29  Munthu woipa amakhala ndi nkhope yamwano,+ koma wowongoka mtima ndi amene njira zake zidzakhazikike.+ 30  Palibe nzeru kapena kuzindikira kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.+ 31  Hatchi* anaikonzera tsiku la nkhondo,+ koma Yehova ndiye amapulumutsa.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”