Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 20:1-30

20  Vinyo ndi wonyoza.+ Chakumwa choledzeretsa chimasokosera+ ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.+  Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+ Aliyense woputa mkwiyo wake akuchimwira moyo wake womwe.+  Kuleka kukangana kumabweretsa ulemerero kwa munthu,+ koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+  Chifukwa cha kuzizira, waulesi salima.+ Iye azidzapemphapempha nthawi yokolola koma sadzapatsidwa kanthu.+  Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,+ koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.+  Pakati pa anthu ambiri, aliyense amanena za kukoma mtima kwake kosatha,+ koma munthu wokhulupirika ndani angam’peze?+  Munthu wolungama amayenda ndi mtima wosagawanika,+ ndipo ana ake amakhala odala.+  Mfumu imakhala pampando wachiweruzo+ n’kubalalitsa zoipa zonse ndi maso ake.+  Ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga,+ ndadziyeretsa ku tchimo langa”?+ 10  Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+ 11  Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.+ 12  Khutu lakumva ndiponso diso loona, zonsezi anazipanga ndi Yehova.+ 13  Usamakonde tulo kuti ungasauke.+ Tsegula maso ako kuti ukhale ndi zakudya zambiri.+ 14  Wogula amati, “Chinthu ichi n’choipa. N’choipa ichi!” Akatero amachoka.+ Kenako amakadzitama.+ 15  Pali golide komanso miyala yamtengo wapatali ya korali yambirimbiri, koma milomo yodziwa zinthu ndiyo ziwiya zamtengo wapatali.+ 16  Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo,+ umulande chovala chake. Ndiponso wochita zoipa ndi mkazi wachilendo umulande chikole.+ 17  Munthu amasangalala ndi chakudya chimene wachipeza mwachinyengo,+ koma pambuyo pake, m’kamwa mwake mumadzaza miyala.+ 18  Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana,+ ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+ 19  Woyenda uku ndi uku n’kumanena zoipa za anthu ena amaulula zinsinsi,+ ndipo usamagwirizane ndi munthu wotengeka ndi milomo yake.+ 20  Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ 21  Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba,+ tsogolo lake silidzadalitsidwa.+ 22  Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+ Khulupirira Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+ 23  Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndi yonyansa kwa Yehova,+ ndipo sikelo yachinyengo si yabwino.+ 24  Mayendedwe a mwamuna wamphamvu amachokera kwa Yehova,+ koma kodi munthu wochokera kufumbi angazindikire bwanji njira yake?+ 25  Umakhala msampha munthu wochokera kufumbi akathamangira kufuula kuti, “N’zoyera!”+ koma pambuyo polonjeza+ n’kumafuna kuganiziranso bwino.+ 26  Mfumu yanzeru imabalalitsa anthu oipa,+ ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira.+ 27  Mpweya+ wa munthu wochokera kufumbi ndiwo nyale ya Yehova. Imafufuza mosamala mkatikati monse mwa mimba.+ 28  Kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi zimateteza mfumu,+ ndipo chifukwa cha kukoma mtima kosatha kumeneko mfumu imakhazikitsa mpando wake wachifumu.+ 29  Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo,+ ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.+ 30  Zilonda zobwera chifukwa chomenyedwa zimachotsa zoipa,+ ndipo zikwapu zimafika mpaka mkatikati mwa mimba.+

Mawu a M'munsi

Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.