Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 19:1-29

19  Wosauka amene akuyenda ndi mtima wosagawanika ali bwino kuposa munthu wa milomo yopotoka,+ komanso munthu wopusa.  Ndiponso, si bwino kuti munthu akhale wosadziwa zinthu,+ ndipo woyenda mofulumira ndi mapazi ake akuchimwa.+  Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake, choncho mtima wake umakwiyira Yehova.  Chuma chimachulukitsa mabwenzi,+ koma munthu wonyozeka amalekanitsidwa ngakhale kwa bwenzi lake.+  Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo wolankhula mabodza sadzapulumuka.  Anthu amene amakhazika pansi mtima wa munthu wolemekezeka ndi ambiri, ndipo aliyense amakhala bwenzi la munthu wopereka mphatso.+  Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+ komanso anzake amatalikirana naye kwambiri.+ Iye amafuna kuwachonderera, koma iwo amamuthawa.+  Munthu amene wapeza mtima wanzeru+ akukonda moyo wake. Wopitiriza kusonyeza kuzindikira amapeza zabwino.+  Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+ ndipo wolankhula mabodza adzawonongedwa.+ 10  Aliyense wopusa sayenera moyo wawofuwofu. Ndiye kuli bwanji kuti wantchito alamulire akalonga! 11  Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake,+ ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola. 12  Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.+ 13  Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake, ndipo mkazi wolongolola ali ngati denga* lodontha limene limathawitsa munthu.+ 14  Cholowa chochokera kwa makolo ndicho nyumba ndi chuma, koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova. 15  Ulesi umachititsa tulo tofa nato,+ ndipo munthu waulesi amakhala ndi njala.+ 16  Wosunga lamulo akusunga moyo wake.+ Wosasamala za njira zake adzaphedwa.+ 17  Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+ 18  Langa mwana wako padakali chiyembekezo, ndipo usalakelake imfa yake. 19  Wamkwiyo waukulu ayenera kulipitsidwa, chifukwa ukam’pulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri. 20  Mvera uphungu+ ndipo utsatire malangizo* kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo. 21  Mumtima mwa munthu mumakhala zolinga zambiri, koma zolinga za Yehova n’zimene zidzakwaniritsidwe. 22  Chinthu chosiririka mwa munthu wochokera kufumbi ndicho kukoma mtima kwake kosatha, ndipo munthu wosauka ali bwino kuposa munthu wonama.+ 23  Kuopa Yehova kumapezetsa moyo.+ Munthu amagona mosatekeseka+ ndipo zoipa sizim’gwera.+ 24  Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera,+ koma n’kulephera kulibweretsa pakamwa.+ 25  Menya wonyoza kuti wosadziwa zinthu achenjere.+ Ndipo womvetsa zinthu uyenera kum’dzudzula kuti adziwe zinthu zowonjezereka.+ 26  Wochitira zoipa bambo ake ndiponso wothamangitsa mayi ake, ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa. 27  Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo, ndiye kuti wapatuka pa mawu okudziwitsa zinthu.+ 28  Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo, ndipo pakamwa pa anthu oipa pamameza zinthu zopweteka ena.+ 29  Zilango anazikhazikitsira anthu onyoza,+ ndipo zikwapu anazisungira msana wa anthu opusa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “tsindwi.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.