Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 18:1-24

18  Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.+  Aliyense wopusa sakondwera ndi kuzindikira zinthu,+ mpaka zimene zili mumtima mwake zitaululika.+  Mnyozo umabwera limodzi ndi munthu woipa,+ ndipo chitonzo chimabwera limodzi ndi manyazi.+  Mawu a m’kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya.+ Chitsime cha nzeru chili ngati mtsinje wosefukira.+  Kukondera munthu woipa si bwino. Komanso si bwino kukankhira pambali munthu wolungama poweruza.  Milomo ya munthu wopusa imalowa mu mkangano,+ ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+  Pakamwa pa munthu wopusa m’pamene pamamuwononga,+ ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.+  Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga, zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+  Komanso waulesi pa ntchito yake+ ndiye m’bale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+ 10  Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.+ 11  Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba,+ ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.+ 12  Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+ 13  Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.+ 14  Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda,+ koma mtima wosweka ndani angaupirire?+ 15  Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu, ndipo khutu la anzeru limafunafuna kudziwa zinthu.+ 16  Mphatso ya munthu imam’tsegulira khomo lalikulu, ndipo imakam’fikitsa ngakhale pamaso pa anthu olemekezeka.+ 17  Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.+ 18  Maere amathetsa mikangano, ndipo amalekanitsa ngakhale anthu amphamvu. 19  M’bale amene walakwiridwa amaposa mzinda wolimba, ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekera pachipata cha nsanja yokhalamo. 20  Mimba ya munthu imakhuta zipatso za pakamwa pake.+ Iye amakhuta ngakhale zokolola za milomo yake.+ 21  Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime,+ ndipo wolikonda adzadya zipatso zake.+ 22  Kodi munthu wapeza mkazi wabwino? Ndiye kuti wapeza chinthu chabwino, ndipo Yehova amakondwera naye. 23  Munthu wosauka amalankhula mochonderera, koma munthu wolemera amayankha mwamphamvu. 24  Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana, koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.

Mawu a M'munsi