Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 16:1-33

16  Munthu ndiye amakonza maganizo mumtima mwake,+ koma kwa Yehova n’kumene kumachokera yankho la palilime lake.+  Njira zonse za munthu zimaoneka zoyera m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza zolinga zake.+  Pereka ntchito zako kwa Yehova,+ ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.+  Yehova anapanga chilichonse n’cholinga,+ ndipo ngakhale woipa anamusungira tsiku loipa.+  Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.+ Ngakhale anthu atagwirana manja, munthu sangapewe chilango.+  Cholakwa chimaphimbika ndi kukoma mtima kosatha ndiponso choonadi,+ ndipo chifukwa choopa Yehova munthu amapatuka pa choipa.+  Yehova akasangalala ndi njira za munthu,+ amachititsa ngakhale adani a munthuyo kukhala naye pa mtendere.+  Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa mwachilungamo+ kuposa kukhala ndi zinthu zambiri koma mopanda chilungamo.+  Munthu angaganize za njira zake mumtima mwake,+ koma Yehova ndiye amawongolera mayendedwe ake.+ 10  Chigamulo chochokera kwa Mulungu chizikhala palilime la mfumu poweruza milandu.+ Pakamwa pake pazikhala pokhulupirika.+ 11  Muyezo wachilungamo ndiponso masikelo ndi za Yehova.+ Miyala yonse ya m’thumba loyezera kulemera kwa zinthu ndiyo ntchito zake.+ 12  Kuchita zinthu zoipa kumanyansa mafumu,+ chifukwa mpando wachifumu umakhazikika ndi chilungamo.+ 13  Milomo yolungama imasangalatsa mfumu yaikulu,+ ndipo mfumuyo imakonda munthu wolankhula zinthu zowongoka.+ 14  Mkwiyo wa mfumu umatanthauza amithenga a imfa,+ koma munthu wanzeru ndi amene amauziziritsa.+ 15  Nkhope ya mfumu ikawala, zimatanthauza moyo.+ Ndipo mafuno ake abwino ali ngati mtambo wa mvula yomalizira.+ 16  Kupeza nzeru n’kwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+ Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+ 17  Kupewa zoipa ndiko njira ya anthu owongoka mtima.+ Munthu amene amateteza njira yake, amasunga moyo wake.+ 18  Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+ 19  Kuli bwino kukhala wodzichepetsa limodzi ndi anthu ofatsa,+ kusiyana n’kugawana katundu wolanda ndi anthu odzikuza.+ 20  Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino,+ ndipo wodala ndi munthu amene amakhulupirira Yehova.+ 21  Munthu wanzeru mumtima mwake adzatchedwa wozindikira,+ ndipo munthu wolankhula zabwino amakopa ena ndi mawu a pakamwa pake.+ 22  Kuzindikira kumakhala ngati chitsime cha moyo kwa ozindikirawo,+ ndipo malangizo* a anthu opusa ndi uchitsiru.+ 23  Mtima wa munthu wanzeru umamuchititsa kuti asonyeze kuzindikira ndi pakamwa pake,+ ndipo umachititsa milomo yake kutulutsa mawu okopa.+ 24  Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.+ Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+ 25  Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+ 26  Munthu wakhama amadzigwirira yekha ntchito+ chifukwa chakuti pakamwa pake pamamukakamiza kwambiri.+ 27  Munthu wopanda pake amafukula zinthu zoipa,+ ndipo pakamwa pake pamakhala mawu okhala ngati makala amoto.+ 28  Kazitape amangokhalira kuyambitsa mikangano,+ ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.+ 29  Munthu wachiwawa amakopa mnzake,+ ndipo amam’chititsa kuti ayende m’njira yoipa.+ 30  Iye amatsinzinira ndi maso ake pokonza ziwembu.+ Amalumirira mano, ndipo amakwanitsadi kuchita chiwembu. 31  Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero+ zikapezeka m’njira yachilungamo.+ 32  Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu,+ ndipo munthu wolamulira mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.+ 33  Maere amaponyedwa pamwendo,+ koma zonse zimene maerewo amasonyeza zimachokera kwa Yehova.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.